ZOKHUDZA MAPHUNZIRO A za CHIKHULUPILIRO

Ndithu maphunziro ndi chimozi mwazinthu zofunikira kwambiri pokhonza munthu, ndipo ndi chipangizo chokonzera mwana ndi kumpatsira maziko ambali zonse za umoyo wake, kudzera mmaphunziro tingathe kukonza umunthu wa mwana pa kakhalidwe kake ndi anthu a mudzi wake, pa maphunziro ake,pa nzeru zake , pa umoyo wake ndi zina zotero, ndiye tisanakambe za maphunziro achikhulupiliro ndi kufotokoza za kufunika kwake, ndi bwino titadziwa tanthaunzo la maphunziro, kuti amatanthauza chiyani komanso kuti anthu a za maphunziro amafuna chiyani paliwuli?!

TANTHAUZO LA MAPHUNZIRO

Maphunziro ndi ntchito yokhala ndi cholinga komanso yonkera nkera mtsogolo (yopitirira) imene imayendetsedwa ndi malamulo, ndi cholinga chofuna kukonza zikhalidwe za bwino kudzera mukulangiza, kuongolera, kuphunzitsa, kukonza ndi kuyetsetsa kupanga zomwe waphunzirazo. Maphunziro amagwira ntchito ya kusamalira ndikuyang’anira chibadwa cha mwana, ndi kupititsa pa tsogolo maluso ndi zikonzekero za mwanayo, ndi kupangitsa kuti chibadwa chakechi ndi maluso ake aja zikhale zabwino ndi zolongosoka komanso zokwanira ndizoyenera, zomwe zimathandiza kukonza munthu wabwino yemwe angayang’anire dziko la pansi, ndipo maphunziro ndi chida chimene chimapanga utsogoleri mbali zonse za moyo (4) .

KUFUNIKA KWA MAPHUNZIRO A ZACHIKHULIPILIRO

Ndithu chikhulupiliro ndiye cholinga chachikulu chakupezeka chilengedwe ndi munthu, ndipo pa chikhulupiliro ndi pamene pasiyanirana njira paulendo wathu wa dziko la pansi, Allah akulankhula mu Quru’an yolemekezeka kunena kuti “choncho mwaiwo alipo amene adakhulupilira ndipo ena mwaiwo sadakhulupilire”. (Surat Al Baqarah: 253).
Pachikhulupiliro ndi pamene pagona zichito chito za anthu komanso ndichimene chimasiyanitsa kumalo okafikira mu umoyo womwe uli nkudza (5), nthawi ya umwana ndi nthawi imene mwana amatha kusiyanitsa zinthu, chifukwa zimene zimadzalidwa mu nzeru za mwana pa msinkhu umenewu monga: zikhulupiliro, zokonda, zikhalidwe ndi malangizo, zimakhala zovuta kusintha nanji nanji kuchotsera, mwinanso chipsera chake chimatsaliranso pa munthuyo moyo wakewonse (6), pachifukwa chimenechi maphunziro azachikhulupiliro amene amatengedwa iye ali mwana wa mng’ono ndiwo maziko omwe amamanga moyo wa munthu padziko pano.
Ndithu maphunziro kunena mosakuluwika ndikuyikira mtima, popanda kuyikira mtima palibe maphunziro, choyenera kuyikira mtima kwambiri pa maphunziro ndiye kudzala chikhulupiliro, ife tili munyengo yomwe chidwi cha anthu ofufuza za maphunziro chakhamukira kumaphunziro kumbali ya nzeru ndi thupi, ndipo anthu ambiri sakulabadira zamaphunziro ambali ya chikhulupiliro, kafukufuku wawo amalunjika ku zakupambana pa dziko lapansi poona zinthu zooneka ndi maso, popanda kuyikira mtima ndi kukonza zinthu zoti zikamuthandize komanso akasangalare ku umoyo umene uli mkudza, zimene zimapangitsa kuti kuona kwathu pa maphunziro kukhale kosiyana kwambiri ndi iwowo kumabali imeneyi (7).
Zachidziwikireni kuti maphunziro achikhulupiliro pa chisilamu ndi imodzi mwa nsanamira imene inamanga maphunziro munyengo ya mtumiki yoyera, monga mmene tikumvera nkhani kuchokera kwa mwana wa Umaru (r.a) iye adati ndinamumva mtumiki (saw) akunena kuti: “ wina aliyense mwa inu ndi muyang’ayaniri, ndipo aliyense wainu ali ndi udindo pa chimene akuyang’aniracho,mtsogoleri ndi muyang’aniri ndipo ali ndi udindo pa zimene akuyang’anirazo, nayeso mzimayi ndi muyang’aniri wa nyumba ya mwamuna wake ndipo ali ndi udindo pa zimene akuyang’anirazo” (8).

Apa mtumiki akufotokoza zakukula kwa udindo womwe aliyense mwa ife wasenza, ndipo udindo umenewu – palibe kuchitira mwina – ndi wokhudzana kuti wapanga chani kwa anthu amene ali pansi pako? Palinso mau ena amene mtumiki (saw) ananena kuti: “Kapolo wina aliyense yemwe mulungu wampatsa owayang’nira ndiye sanawasamalire moyenera, sakalinunkha fungo la ku Jannah” (Bukhar -7150),
Apa zikuonetsa kufunikira kopereka malangizo mwachilungamo ndi mokhulupilika kotero pafunika langizo lizikhala losayang’ana mbali ndi lokomera olangizidwayo kumbali zonse, mwankhani zina zimene zinabwera pa mutuwu ndi mau amwana wa umaru (r.a) onena kuti:“Umuphunzitse chikhalidwe mwana wako chifukwa ndi udindo wako pa iyeyo kuti unamuphunzitsa khalidwe lanji? Komanso wamuphunzitsa chiyani? Nayenso ali ndi udindo wokuchitirani inuyo ubwino ndi kukumverani malamulo anu” (9).

Apa mwana wa Umaru akutsindika kuti udindo umenewu poyamba umakhala pa makolo, chifukwa iwowo ndigwero limene ana amapezera maphunziro ndi chikhalidwe, ndipo mu hadith ina ananena kuti maphunziro ndi abwino kuposa kupereka chaulele, chifukwa zanenedwa kuti “munthukuphunzitsa mwana wako chikhalidwe ndi kwabwino kuposa kupereka cha ulere cholemera ma kilogalamu awiri ndi theka(2.5kg) azakudya (10). Komanso pali hadith ina yomwe imati: “kuphunzitsa mwana chikhalidwe chabwino ndi kwa bwino kuposa kupereka china chilichonse mwa ulere”, inaso ikuti: “kholo silingathandize mwana wake ndi chinthu cha pamwamba kwambiri choposa kumuphunzitsa chikhalidwe chabwino” (11). Maumboni onsewa ndi ena otero akusonyeza kuti kuikira mtima pa kuphunzira ndi kuphunzitsa ndi chimodzi mwazinthu zikulu zikulu zofunikira zomwe makolo angapereke Kwa ana awo.

Ndiye kale ana timawalera munjira yotsekeka mbali ina, koma lero tikumawalera kumachita kuti makomo ndi mazenera anyumba zathu ali otsekukira kudziko lapansi kuchokera ku mapeto adziko mpaka kumapeto, zimenezi mwachikhalire zimakhala ndi ubwino ndi kuyipa, moti tikapanda kuchenjera ndikuzimvetsa bwino zimene zikuyendazo, ndiye kuti zoipazo zitha kuononga zabwinozo, tingathe kumvetsa zizindikiro za kusintha kwa makono ngati tikhala ndi chidwi pa kusinthasintha kwachangu komwe kukuchitika panopa ndi kukuwerenga bwino (kusinthako) pogwiritsa ntchito maphunziro, zimenezi zimapangitsa iye uja kuti adzadzitse matanthaunzo achikhulupiliro m’mitima ya ana kudzera mu umoyo wapa banja womwe banja lonse limafuna, komanso kudzera mukuwasakira ana masewero ndi masukulu omwe amayikira chidwi pa zimenezi, kusazimvetsa zomwe zikuyenda zimapangitsa kuti uluze kuluza kwake kokanika nako kubwezeretsa (12). Koma kudzera mmaphunziro opitilira, ndi (kudzera mu) kupilira kosalekeza; titha kupeza zotsatira zapamwamba zambiri – muchifuniro cha Allah-. Pamaphunziro sizimakwanira kulangiza ndi kusiyira pompo ayi, koma zimafunika kutsatira ndi kulangiza mosalekeza (13).

MAPHUNZIRO A ZACHIKHULUPILIRO NGOFUNIKA ZEDI

Anthu am’bado uno amafuna kutchuka iwo eni ndi kutchukitsa chikhalidwe chawo (culture) ndi kukhala ndi chili chonse, koma zomusokoneza zomwe zamuzungulira mbali zake zonse ndi zoopsa kwambiri komanso ndizoyenera kuzilingalira, ndipo ife timagwira ntchito yovuta kwambiri pa anthu, ntchito yake ndiya maphunziro (14). Zina mwa zimene zikusonyeza kufunikira kwa maphunziro achikhulupiliro kwa ana ndi kusowekera kwa maphunziro amenewa kwa anthu: ndi kuti kuonetsa chidwi pophunzitsa anthu maphunziro achikhulupiliro ndi kuwayitanira kuchimenecho makamaka ana ndiwo mchitidwe wa atumiki _ madalitso ndi mtendere zikhale pa iwo– ndi anthu olungama omwe anabwera pambuyo pa iwo, zina mwaizo ndi mawu MAPHUNZIRO A ZACHIKHULUPILIRO ngoFUNIKA zedi amene akulankhula Allah zokhudza Nowa (Nuhu) (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) m’mene amaitanira mwana wake ndi kumuchenjeza zoyenda ndi anthu osochera Allah akunena kuti Nowa adati kwa mwana wake: Mwana wanga! Kwera pamodzi ndi ife usakhale pamodzi ndi osakhulupilira” (surat Hud :42) Komanso Allah akulankhula zokhudza Ibrahim pa nthawi imene amawalangiza ana ake, Allah akunena kuti: “Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi chonchonso Yakubu (adalangiza ana ake kuti) E. inu ana anga! Ndithu mulungu wakusankhirani chipembedzo (cha chisilamu) choncho musafe pokha pokha muli asilamu (ogonjera iye)” (Surat baqarah: 132)

Komanso langizo loyamba la Luqman pamwana wake anamuchenjeza za shirik ndipo Allah akunena kuti “Ndipo (akumbutse) pamene Luqman adauza mwana wake akumulangiza Ee! iwe mwana wanga! Usaphatikize Mulungu ndi mafano. Ndithu, kumuphatikiza (Mulungu) ndi zinthu zina ndi kuipitsa kwakukulu” (Surat Luqman: 13).

Nayeso mtumiki Muhammad (saw) analangiza mwana wa Abbas (r.a) kunena kuti “oh! mwana iwe, ndikufuna ndikuphunzitse mau awa: Samala malamulo amulungu ndipo iye adzakusamala, umusunge Mulungu ndipo iye udzamupeza patsogolo pako, ukafuna kupempha uzipempha Mulungu, ukafuna thandizo uzimupempha Mulungu” (Tirmizi -2516). Mulangizo limeneli muli kuonetsa chidwi pamaphunziro azachikhulupiliro.

Mwazinanso zimene zikusonyeza kufunikira kwa maphunziro ndi: podziwa kuti kuphunzitsa chikhulupiliro ndiye phata la maphunziro onse, ndiye mwana akaphunzira maphunziro achikhulupiliro nadzalidwa mu mtima mwakemo mogwirizana ndi ndondomeko ya atumiki, ndiye kuti mapemphero ena onse ndi nthambi zina za chipembedzo zimatsatira pambuyo pake, ndipo kuikira chidwi ndichifukwa chimodzi chopezera chiongoko – muchifuniro cha Mulungu -, chifukwa malamulo ambiri amangidwa (amayenda) ndi chikhulupiliromwa Allah ndi tsiku lomaliza, ndiye chikhulupiliro chikakhala ndi mphamvu, chimamuletsa munthu uja njira yoletsedwa.

Chinanso chimene chikuonetsa kufunikira kwa maphunziro: ndikusalabadira komwe tikukuona mwa makolo ena posaphunzitsa ana awo zokhudza chikhulupiliro pogwiritsa umboni wonena kuti akadali achichepere, ngakhale akamakula samathanso kuwaphunzitsa. Yemwe angazengereze zophunzitsa mwana wake zinthu zomwe zingamuthandize namutayilira ndiye kuti wapanga chinthu choipitsitsa. Ana ambiri kusokonezeka kwao kumachokera kwa makolo awo ndi kusalabadira kwawo ( makolo ) posawaphunzitsa zinthu zimene zili zokakamizika pa chipembedzo ndi zichito chito zamtumiki (Sunnah), ndipo amawaononga ali aang’ono moti anawo amakhala kuti sanapindule ndipo sangathandize makolo awo ku ukulu (15).

Chinanso ndi kuchuluka kwa mapologaramu okhudza ana mu njira ya mauthenga (monga: zoonerera, zomverera ndi zowerengedwa), zomwe zimafalitsa kwambiri zithunzithunzi ndi matanthaunzo osokoneza mmitima ya ana, ndiye pakufunikira kwambiri kuti papezeke maphunziro azachikhulupiliro omwe angalimbane ndi mauthenga amenewa, ndiye maphunziro adza chikhulupiliro amagwiritsa ntchito zipangizo zimene zili zovomerezeka mchipembedzo, ndipo zimateteza mwana mokwanira ku mavuto onse apa maphunziro asanachittike, komanso amathandiza kuwachiza mavutowo akachitika, izi ndizofunikira kwambiri kuti makolo awachitire ana awo komanso zimabweretsa chisangalalo padziko lapansi pano, komanso ndi kukapeza chipulumutso pa umoyo umene uli nkudza – muchifuniro cha Mulungu-, ndipo icho ndi chifukwa chomwe chidzasiyanitse anthu tsiku la chiweruzo (16).

Chomaliza maphunziro a zachikhulupiliro amabweretsa kukhazikika ndi mtendere wa mmitima ya ana; chifukwa zimabweretsa mayakho amafunso akulu akulu apa umoyo, izi zimachitika kamba kathandizo la buku lolemekezeka.

ZOLINGAZA MAPHUNZIRO AZA CHIKHULUPILIRO

Ndithu cholinga chachikulu chamaphunziro ndiko kukwanilitsa ukapolo weni weni pa Mulungu, choncho cholinga chimenechi chimafuna kukwanilitsa zolinga zina zing’ono zing’ono zochuluka, zina mwaizo:

Choyamba: kukhazikitsa chikhulupiliro cholondola pa ana a dera la chisilam; pofuna kukhonza munthu wolungama yemwe azipembedza Mulungu wa pamwamba movomereza ndi mozindikira.

Chachiwiri: kuti munthu akhale m’dera la chisilam ndi chikhalidwe chabwino motsatira makhalidwe amtumiki (saw) yemwe Mulungu anamuyikira umboni ponena kuti“Ndipo ndithu uli nawo (iwe Muhammad) makhalidwe abwino kwambiri” (Surat Qalam: 4), komanso pogwiritsa ntchito mawu amtumiki onena kuti: “Ndithu ndinatumizidwa padzikoli kudzakwanilitsa makhalidwe abwino” (18).

Chachitatu: kukhazikitsa umodzi pakati pa asilamu; chifukwa munthu uja amadzimva kuti iye ndi mmodzi mwa anthu adelaro ndiye kuti amalumikizana ndi azinzake pogwiritsa ntchito mau a Mulungu onena kuti: “Ndithu, okhulupilira onse ndi pachibale choncho yanjanitsani pakati pa abale anu ndipo muopeni Mulungu kuti akuchitireni chifundo” (Surat Al- hujirat: 10), ndi mawu ochokera kwa mtumiki onena kuti: “wokhulupilira pa wokhulupilira nzake ali ngati nyumba yomwe chipupa china chimalimba kamba ka chipupa chinzake” (Bukhar -6026), komanso anati: “mupeza anthu okhulupilira pakumverana chisoni kwao, ndi pa chifundo chawo, ndikukondana kwao ndi kufewerana kwa mitima yawo, alingati thupi limodzi, ngati chiwalo chimodzi chitadwala thupi lake lonse limathandizira kuchezera ndi kunjenjemera” (Bukhar -6011). Kudzera muzimenezi ubale wa chikhulupiliro umamangika pakati pa asilamu.

Chachinayi: kukhonza munthu wolongosoka m’maganizo ndi mumtima momwe, zimenezi zimathandiza kukhonza munthu waphindu mudera la asilamu. Yemwe angakwanitse kugwiritsa ntchito maudindo ake pakutukula ndi kupititsa patsogolo zabwino za dzikoli, ndikugwirantchito yolemetsa ndi yofunikira ya utsogoleri yomwe Allah anamuyikira munthu (Adam) padzikoli (19).
Kuchokera pa zimenezi; pakuonekera kufunikira koyamba kwa maphunziro achikhulupiliro – cheni cheni -, omwe amagwira ntchito popereka mphamvu za uzimu, ndikulimbitsa chitetezo cha thupi ndikuyika uzimu muzolankhula ndi zichitochito zawo ndiye kuchokera pazimenezi zimakhala zophweka kwa munthu kugwira ntchito zofunikira pofuna kukwaniritsa zolinga za maphunziro akuzindikira wamba (theory) ndi a zichitochito (practical) (20).

Maziko A MAPHUNZIRO

Pali ngodya zomwe zimayezamilidwa pomanga maphunziro, zomwe tingathe kuzisonkhanitsa mungodya ziwiri zikulu zikulu, yoyamba: ngodya yakuzindikira wamba (theory), ndipo yachiwiri ndi ngodya ya ntchito (practical).

Ngodya ya kuzindikira imeneyi itha kugawidwanso pawiri:
1- Maphunziro
2- Chikhulupiliro

Gawoloyamba: Maphunziro: gawo ili limatengedwa ngati kiyi wamkulu kwambri yomvetsetsera zinthu komanso ndikumangira ndi kutetezera chikhalidwe, ndipo Allah akunena kuti“Nena (kwa iwo iwe mtumiki) “kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa ngofanana”? (Surat Azumar: 9)..
Ndithu mtumiki (saw) anayetsetsa kuphunzitsa ophunzira ake maphunziro aphindu, komanso anawaphunzitsa kuti azimupempha Allah kuti awateteze kuchokera kumaphunziro opanda phindu, moti anati muduwa (pempho) yomwe amawaphunzitsa maswahabawo: “O! Allah ine ndikuzitchinjiriza ndi kupempha chitetezo mwainu kuchokera kumaphunziro opanda phindu ndi mtima wosaopa Allah. (Muslim – 2722).

Gawolachiwiri: Chikhulupiliro: ichi ndi chomwe chimakhazikika m’mitima ya ana monga kukhulupilira nsanamira zisanu ndi imodzi za chikhulupiliro, limenelo ndi tanthaunzo losonkhanitsa zomwe zili mu umoyo uno ndi umoyo womwe uli nkudza. Ndipo mtumiki (saw) anaonetsa chidwi pofuna kudzala chikhulupiliro cholongosoka m’mitima ya ummah (anthu) wake.

Pomwe ngodya ya ntchito (practical) itha kugawikana patatu
1- Kupembedza.
2- Kukwanilitsa (ntchito).
3- Chikhalidwe.

  1. Gawo loyamba: kupembedza (21), maphunziro aphindu amafunika azimukhonza munthu pachikhulupilro chabwino komanso azimupatsa mbiri zapamwamba, zomwe zingamange umunthu wa ana ndicholinga choti akhale woyera mtima ndi wolumikizana kwambiri ndi Mulungu wake, nakhala wachikhalidwe ndi maganizo olungama, ndikukhala zolingalira zake zolongosoka, pachifukwa chimenechi mtumiki (saw) anamuuza Muadhi bun Jabal kuti ndikulumbira mwa Allah kuti ine ndimakukonda, ndiye usamasiye pambuyo pa swala ili yonse kunena mau oti “O, Allah ndithandizeni ine kuti ndizikukumbukirani pafupipafupi ndikukuyamikani ndikukupembedzanimoyenerera” (Abu Daudu – 1522).
    Apa mtumiki anamuphunzitsa iye kuti kupembedza ndi mphatso ya pamwamba yochokera kwa Mulungu, osati chifukwa cha kulimbikira kwa munthu kokha ayi, koma chifukwa cha kuthekera kwa Allah (taufiiq), komanso anamuphunzitsa kuti mapemphero amafuna nthawi zonse chithandizo chochokera kwa Mulungu, ndiye zikhazikike mu mtima mwakemo kuti munthu wokhulupilira akukakamizidwa kuti akamamupembedza mbuye wake azimupempha thandizo ndikumuyezamira iye, chifukwa iye Mulungu ndi amene amapereka kuthekera komumvera malamulo ake.
  2. Gawolachiwiri: Nchito (practical): palibe maphunziro ngati sakutsatilidwa, ndiye ntchito ndi chida chomwe chikawapambanitse anthu ena ku umoyo umene uli mkudza, Allah akunene kuti “Choncho, amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake. Ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake (Mulungu sachitira chinyengo aliyense). (Surat az zalzalah: 7-8).
  3. Gawolachitatu: Makhalidwe: ndondomeko yachisilamu imakonza munthu kakhala ndi khalidwe labwino, mpakana mtumiki mwini wake amaona kuti uthenga wake wonse ukuzungulira pa tanthaunzo limodzi lomwe ndi khalidwe labwino, ndikuphunzitsa khalidwelo, ndipo anati: “Ndithudi ndinatumizidwa kudzakwanilitsa makhalidwe abwino” (Ahmad – 8939), ndipo analimbikitsa za makhalidwe abwino m’mau ake onena kuti: “Ndithu okondedwa kwambiri mwainu kwaine komanso wachifupi kwambiri mwa inu kwaine tsiku lachiweruzo; ndi okhawo amene ali ndi makhalidwe abwino” (Tirmizi – 2018), choncho kukhala ndi makhalidwe abwino ndilo phindu la maphunziro a zachikhulupiliro loonekera ndi zotsatira za maphunziro a za chikhulupiliro

ZITSANZO ZOCHITIKA ZOPHUNZITSA

Ndithu kupereka zitsanzo za ntchito (practical) ndi chimodzi mwazithu zomwe zimathandiza kulimbitsa maziko ndi zikhulupiriro, ndiye pano tibweretsa mwachidule zambiri mwazitsanzo zomwe zimafotokoza m’mene chiphunzitso cha mtumiki chinalili ndi ophunzira ake pomanga chikhulupiliro pa ana (24)

  1. Nkhani inachokera kwa mwana wa Abbas (r.a) iye adati: Anali mtumiki akuwapemphera chitetezo Hassan ndi Hussein ndipo amanena kuti ndithu bambo anu (Ibrahim) anali kuwapemphera chitetezo Ismaila ndi Ishaaq kwa Mulungu ndi mau awa: Ndikupempha chitetezo kudzerammau a Allah omwe ali okwanira kuti asandifikire satana aliyense ndizoipa zina zilizonse komanso kuti lisandifikire diso lamatsoka (Bukhar – 3371)..
  2. Adanenanso Abu Huraira (r.a) kuti iye adamumva mtumiki (saw) akunena kuti: “Mwana wina aliyense amabadwa ali ndi chikhulupiliro choti Mulungu ndi modzi, koma makolo ake ndi amene amapangitsa kuti (mwanayo) akhale muyuda, mkirisitu kapena wopembedza moto (mafano)” (Bukhar – 1358).
  3. Ndipo Umaru mwana wa Abi Salama akunena kuti: tsiku lina ndili mwana mnyumba ya mtumiki (saw), unali mkono wanga ukuyendayenda paliponse mumbale ya chakudya ndiye mtumiki anandiuza kuti: “Ee! mwana iwe, umutchule kaye Allah, ndipo uzidyera dzanja lako lakumanja ndipo uzidya mbali yako”.(Bukhar – 5376, Muslim – 2022)
  4. Mwana wa Abbas(r.a) ananenanso kuti: tsiku lina ndinali pambuyo pa mtumiki (saw) ndiye mtumiki anandiuza kuti: “E, mwana iwe, ine ndikuphunzitsa mawu awa: Umusunge Mulungu ndipo iye adzakusunga, umusunge Allah ndipo udzamupeza patsogolo pako, ukafuna kupempha uzimupempha Allah, ukafuna kupempha chithandizo uzimupemphanso Allah, dziwa kuti anthu onse atati asonkhane kuti akuthandize china chake sangakwanitse kupatula pachimene Allah anakulembera”. ( Tirmiz – 2516).
  5. Ndipo Hassan mwana wa Allie (r.a) anati: anandiphunzitsa mthenga wa Allah mau oti ndiziwalankhula mu dua ya qunoot ya witri) kuti ndiziti: “O Allah ndiongoleni ine mundiyike mgulu la anthu omwe mudawaongola, nditetezeni kuzoipa pondiyika mugulu la amene munawateteza, ndiyang’anireni mundiyike mugulu la amene mumawayang’anira, ndidalitseni pa zimene mumandipatsa, ndipo nditchingireni zoipa zimene munazikonza kuti zindipeze, ndithu inu ndi amene mumayika zikonzero pa ife ndipo palibe amene angatero pa inu, ndithu sanganyozeke yemwe mwamuyang’anira inu (Allah), ndipo sangalemekezeke yemwe mwadana naye,mwayeretseka inu mbuye wathu Allah komanso ndinu wapamwambamwamba” (Abu Daudu – 1425).
  6. Anasi mwana wa Malick adati: mtumiki wa Allah adandiuza kuti “Ee! mwana wanga, ukamalowa mnyumba muli mkazi wako; uzipereka salaam, zikubweretsera madalitso iweyo ndi apa banja lako” (Tirmizi – 2698).
  7. Jumdubi wa fuko la bujari (r.a) adati: Tidali ndi mtumiki (saw) tili anyamata achisodzera, tidaphunzira chikhulupiliro tisanaphunzire Quru’an, titaphunzira Quru’an tidaonjezereka nayo chikhulupiliro” (Ibun Majah-61).
  8. Mayi ake a Suleymu Arraymiswaau mayi ake a Anasi bun Malik (r.a) analowa chisilamu mayi amenewa Anasi ali mwana wang’ono, asanasiye kuyamwa, koma mzimayi ameneyu ankamuphunzitsa Anasiyu kuti anene mau awa : “palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Allah yekha” komanso amamuuza kuti anene kuti:“ndikuchitira umboni kuti Muhammad ndi mthenga wa Allah”, ndipo Anasi amanena zimenezi (22).
  9. Ndipo Ibrahim wafuko la taymu (r.a) anati: ophunzira amtumiki (maswahaba) “ankaona kuti ndibwino kuti mwana akangoyamba kulankhula amuphunzitse liwu loti (Laa ilaahaillallah), kutanthauza kuti (palibe winawomupembedza mwachoonadi koma Allah yekha) kasanu ndi kawiri -, ncholinga choti zimenezo zikhale zoyambirira kuziyankhula mwanayo (23).
Back to top button