ZITSANZO ZA MMENE TINGAYANKHIRE MAFUNSO A ANA OKHUDZA CHIKHULUPIRIRO
Ndipo pofuna kuyankha mafunso a mwana okhudza chikhulupiriro, makolo akuyenera kukhala ndi mlingo wokwanira wa maphunziro a chipembedzo wowaloleza iwo kupereka matanthauzo oyambirira omwe angawafotokozere ana awo zinthu zobisika mwa njira yolingana ndi nzeru ndi kuthekera kwa anawo, ndipo zovuta zomwe a zamaphunziro amakumana nazo si kusonkhanitsa maphunziro kokha ayi, koma kuwaika (maphunzirowo) mukakhalidwe koti nzeru za anawo zithe kuwalandira ndi kuwamvetsetsa, komanso kuwabweretsa moyenera ndi nthawi komanso ndi nyengo yomwe mwanayo amakhala.
Ndipo zikubwerazi ndi zina mwa zitsanzo za mafunso omwe amabwerabwera pa lilime la ana, ndipo dziwani kuti awa simafunso onse ayi, koma ofunikira kwambiri mwa iwo ndiponso omwe amafunsidwafunsidwa kwambiri, ndipo tayesetsa kuika mayankho abwino kwambiri okha okha malinga ndi kuona kwathu, ndipo sitikudzichemerera kuti amenewa ndi mayankho apamwamba kwambiri ayi; koma kuti izo ndi zitsanzo zoti makolo atha kuzitenga ngati poyambira, ndipo tikukutsimikizirani kuti mayankho amenewa mutha kuwakonza, kuwapungula kapena kuwaonjezera.
CHENJEZO: Yemwe angaganize kuti iye sangakwanitse kuphunzitsa ana ake, kuopera kukumana ndi mafunso ovuta; ndiye kuti iyeyo ndi wolakwitsa, khalidwe limenelo ( lokonda kufunsa mafunso ovuta) kwa ana ndi chizindikiro cha thanzi lawo kuti akukula mwa chilengedwe komanso kuti nzeru ndi kuthekera kwa kuganizira kwawo kukukula mwa dongosolo, ndi kuti pakapezeka vuto, ndiye kuti ndi chifukwa cha kulephera makolo kukwaniritsa makulidwe a mwana wawo ndi kulephera kutsegula ngodya za nzeru zake ndi kulandira kwake zinthu zobisika ndi zooneka zomwe zamuzungulira (126). Choncho makolo ndi aliyense yemwe amayanganira mwana adzayenera kulimbikira kumpatsa mwanayo mayankho ogwira mtima olo kangachepe, chifukwa yankho logwira mtima pang’ono limathandiza kudekhetsa mtima wake, maganizo ake ndi kukhala kwake ndi anthu, pomwe mayankho olakwika amaonjezera mwana kubalalika, ndipo kubalalika kumeneku kumapangitsa kusokonekera kwa khalidwe la mwanayo, ndi kuperewera kuganiza kwake komanso kachitidwe kake ka zinthu.
Ndithu mavuto akulu akulu samadza nthawi imodzi, olo moto umayamba ndi lawi lalingono, choncho; makhalidwe ambiri oyipa pa munthu amaoneka ngati njere yayingono yothiriridwa ndi kuzengereza ndi kuimikira imikira, ndipo kamakulirakulira kamba ka kusalabada chifukwa chotengeka ndi umoyo mpaka kukula namerera mizu mu mtima moti siingatheke kuchoka kapena kuzulidwa (127).
Amenewa adali ambiri mwamafunso omwe amafunsidwa funsidwa, ndipo ife tikukulandirani kuti munthu akafuna kulumikizana nafe apeze (Lumikizanani) yathu kuchokera kwa sheikh wathu uyu (Adams Maxwell) pakafunika mayankho amafunso ena, kapena mukafuna kupereka zitsanzo zina zabwino kwambiri kuposa zimene tabweretsazi. .