MAFUNSO A ANA PA CHIKHULUPILIRO

Ndithu chipembezo pa mwana chimayamba ndi ganizo limodzi – ganizo lake la kupezeka kwa Allah-, kenako amayamba kuonekera m’maganizo ena- monga ganizo la kulenga kapena lokudza umoyo umene uli nkudza, kapena Angelo, kapena ziwanda (asatana).

MAU OYAMBA

zaka zoyambilira za umwana zili ndi ubwino wa ukulu pokonza m’mene mwana azionera chilengedwe, chifukwa chithunzi thunzi chomwe chimadzalidwa mu nzeru za mwana mu nyengo imeneyi, chimatengedwa ngati mwala wa maziko womwe umakonza umunthu wa mwanayo kumbali zake zonse (zosiyana siyana) ndipo umafunikira (mwalawo) kuti uziyendera limodzi ndi zofunikira za mwanayo zokhudza umoyo, chikhalidwe ndi chipembedzo, zomwe zingamuthandize mwanayo kuti ayambe mwa mphamvu ulendo wake wolowa mu zipsinjo ndi mikwingwirima ya umoyo (mavuto) ndi kudutsamo molongosoka ali munthu waphindu komanso wothandiza kudzera mu zimene akumazimva ndi kuziona, amakonzanso chitsanzo chake chake chadzikoli, kotsala kwa moyo wakeko pambuyo pa zimenezi kumangokhala kukonza kapena kupititsa patsogolo chithunzi thunzi chake choyambilira chija potengera nyengo zimene akudutsana nazo.

TANTHAUZO LA MAPHUNZIRO

Maphunziro ndi ntchito yokhala ndi cholinga komanso yonkera nkera mtsogolo (yopitirira) imene imayendetsedwa ndi malamulo, ndi cholinga chofuna kukonza zikhalidwe za bwino kudzera mukulangiza, kuongolera, kuphunzitsa, kukonza ndi kuyetsetsa kupanga zomwe waphunzirazo. Maphunziro amagwira ntchito ya kusamalira ndikuyang’anira chibadwa cha mwana, ndi kupititsa pa tsogolo maluso ndi zikonzekero za mwanayo, ndi kupangitsa kuti chibadwa chakechi ndi maluso ake aja zikhale zabwino ndi zolongosoka komanso zokwanira ndizoyenera, zomwe zimathandiza kukonza munthu wabwino yemwe angayang’anire dziko la pansi, ndipo maphunziro ndi chida chimene chimapanga utsogoleri mbali zonse za moyo (4) .

Werengani zambiri

Sikuti maphunziro ndiye kungokonza zolakwika zokha ayi, koma kuphunzitsa ndi kupereka maziko a chipembezo ndi malamulo a chisilam ndi kugwiritsa ntchito njira zosiyana siyana monga kukhazikitsa zithuzi thuzi (za zomwe ukumuphunzitsa) ndi kuzipangitsa zimenezo kuti zikhazikike mmitima mwawo – monga kuphunzitsa kudzera mukuonera kwa ena, ulaliki, nkhani, zochitika,ndi zina zotero; ncholinga choti titulutse munthu wolongosoka komanso waphindu pa umoyo komanso pa mudzi ( pa malo).

Kodi Allah (MULUNGU) ndi ndani?

Choyamba, tisadikire kuti mpakana mwana atifunse zokhudza Allah,koma timufotokozere mwachangu za Allah nthawi zonse komanso pa zochitika ndi pampata (opportunity).

Kodi Allah amafanana ndi munthu Him?

Ayi safanana naye,iye safanana ndi chilichonse, iye ndi amene analenga ine, iweyo ndi anthu onse, analenga mitengo, mitsinje,Nyanja ndichina chilichonse pa dziko lapansi pano, kwa iye ndi kumene kumachokera mphamvu za pamwamba.

Kodi yemwe adamUlenga Allah ndi ndani?

Zikadakhala kuti alipo yemwe adalenga Allah,inenso nkadafunsa kuti: ndani adalenga mlengi? Sichoncho? Kotero tikuyenera kudziwa kuti zina mwa mbiri za mlengi ndi zakuti: iye sadachite kulengedwa ndipo iye ndi amene adalenga zolengedwa zonse, akadakhala kuti iye adachita kulengedwa sitikadamupembedza kapena kutsatira chiphunzitsondi malamulo ake, ndiye funso lonena kuti ndani adamulenga Allah silolondola ndipo lilibe tanthauza.

KODI ALLAH ADACHOKERA KUTI NANGA ALI NDI ZAKA ZINGATI?

ukudziwa kuti Allah sadalengedwe; ndithudi chimodzimodzi iye sadabeleke kapena kubelekedwa, alibenso chiyambi ngakhalenso mathero, kotero alibe zaka zakubadwa ngati momwe zikhalira kwa ife anthu, chifukwa Allah ndiye mlengi wamkulu wolemera kwambiri, mwini mphamvu komanso wolimba, mwini ulemerero ndi wachifundo yemwe ali ndi maina abwino okhaokha ndi mbiri zabwino komanso.

Kodi Allah ndi wamwamuna kapena wankazi

Tikuyenera kuzitalikitsa nzeru za mwana kuti zisamaganizire kwambiri za maonekedwe a Allah, ndipo tiziongolere nzeru zake kuti ziziganizira zinthu zomwe zingamubweretsere phindu, apa tsopano zidzakhala bwino kumuuza momveka kuti kukhala mwamuna kapena mkazi ndi zinthu zosiyanitsira magulu ndi mitundu ya zolengedwa za moyo, izi ndi zina mwa zomwe Allah anazipatsa zolengedwa zake.

MAFUNSO A ANA OKHUDZA CHIKHULUPIRIRO

Bukuli lagawidwa m’magawo awiri : gawo loyamba (zokhudza maphunziro a chikhulupiliro ), m’menemo muli maziko ambiri omwe angathandize makolo kuphunzitsa ana awo – mu chifuniro cha Allah -, pomwe gawo la chiwiri likuzungulira pa (zitsanzo zochitika pakayankhidwe ka mafunso a ana okhudza chikhululupiliro) m’menemo tiyankhamo mafunso amene ali otchuka kwambiri pakati pa ana amisinkhu yosiyana siyana, makamaka omwe akukhudzana ndi msichi zachikhulupiliro zisanu ndi imodzi ndipo tafotokozamo momveka bwino m’mene tingayankhire mafunso ngati amenewa.

Werengani zambiri

Back to top button