MAFUNSO OKHUDZA ATUMIKI

Kodi aneneri ndi atumiki ndi ndani?

Iwo ndi anthu ochokeranso mwa ana a Adam, Mulungu anavumbulutsa kwa iwo utumiki ndipo anawalamula kufalitsa uthenga wa Mulungu kwa anthu awo, ndikuwaitanira kuti adzimupembedza Mulungu yekha. Mneneri woyamba ndi Adam ndipo womaliza wawo ndi Muhammad (saw). Chiwerengero chawo ndi chochuluka kwambiri chifukwa Mulungu amawatumiza iwo ku mibadwo yonse yomwe idapezeka padziko lapansili, moti nyengo iliyonse mumbiri zakale imakhala ndi mneneri wowaitanira anthu ake ndikuwaongolera kunjira yoongoka.

Kodi chifukwa chiyani Mulungu adatumizaatumiki?

Mulungu adatumiza atumiki chifukwa cha chifundo chake pa anthu ndi kufuna kuwaongola, kuti (atumikiwo) afalitse kwa anthuwo uthenga wa mbuye wawo, ndiye mtumiki amakhala munthu yemwe anthu ake amamudziwitsitsa bwinobwino komanso yemwe iwo amaikira umboni za ubwino wake kuyambira asanalandire chibvumbulutso, ndipo Mulungu adawapanga atumiki kukhala chitsanzo chooneka ndi maso pa anthu, amawaphunzitsa iwo kudzera mmakhalidwe ndi zichitochito ndikumawalongosolera zomwe zingamawathandize ndikuwatalikitsira zomwe zingawazunze, moti kutumiza atumiki kunali kuika umboni pazolengedwa zake ndikuwasonkhanitsa anthu pachipembedzo chimodzi chomupembedza Mulungu yekha (155), chifukwa anthu akufunikira wowaongolera kunjira yoona muchilankhulo chawo, pachifukwa ichi Mulungu amavumbulutsa kwa atumiki amenewa mabuku muchiyankhulo cha anthu awo ndicholinga choti uthengawo uwapeze momveka bwino kwambiri.

Kodi aneneriwa samalakwitsa (anali otetezeka ku machimo)?

Anenerinso ndi anthu mwaiwo mulinso matanthauzo aumunthu, Mulungu anawateteza iwo kumbali ya utumiki yokhayo, anawateteza kuti asagwere mu zomwe zingadetse zochita zawo kapena makhalidwe awo, ndicholinga choti akakhale chitsanzo chabwino, anthunso azikhutitsidwa ndi mau komanso zochita zawo, ndinso kuti chisakhale chifukwa chodetsera ntchito yawo yakufalitsa uthenga wa Mulungu, koma ngakhale zili choncho iwo ndi anthunso amatha kulakwitsa kwa wamba kosapereka vuto kuutumiki wawo, monga: kulakwitsa kuyeza malo oyenera kulima kapena a nkhondo, kapena mulingo wachidwi choyitanira anthu kuchipembedzo (156).

Kodi Muhammad ndi ndani?

Iye ndi mneneri womaliza mwa aneneri omwe Mulungu anawatumiza kwa akapolo ake, ndipo dzina lake ndi Muhammad mwana wa Abdullah mwana wa Abdul-muttalib wochokera mwa Hashim wafuko la chiquraish, anabadwira ku makkah, tsiku lolemba mwezi wa Rabiul-awwal, chaka cha Njovu, bambo ake anamwalira iye ali m’mimba mwa mayi ake, mayi ake adamwalira iye ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi (6) zakubadwa, kenako analeredwa ndi agogo ake Abdul- muttalib omwe anadzamwalira mtumiki ali ndi zaka zisanu ndi zitatu (8), kenako anamulera iye amalume ake (bambo ake ang’ono) Abu Taalib, mtumikiyu ankatchedwa “wonena zoona wokhulupilika” chifukwa chakhalidwe lake lapa mwamba, analandira utumiki ali ndi zaka makumi anayi, anakhala akuitanira anthu ake kuchisilamu ku Makkah kwa zaka khumi ndi zitatu (13), kenako anthu aja atamuzunza kwambiri iye anasamukira ku Madina nakakhazikika kumeneko kwazaka khumi, analumikiza kumeneko ubale pakati pa asilamu ochokera ku Makkah ndi aku Madinako, Ndipo anakhazikitsa kumeneko malamulo a Mulungu, ndipo adamwalira kumeneko muchaka cha khumi ndi chimodzi chisamukireni kuchokera kuMakkah, komanso pambuyo pofalitsa uthenga wa Mulungu mokwanira ndikubweza kwa anuwake zonse zomwe anasungitsidwa (157).

Kodi nchiyani chomwe chingatsimikizire zoti mtumiki Muhammad amanena zoona zokhazokha?

Maumboni osonyeza kuti Muhammad ndi mtumiki ndi ambirimbiri, ndipo ofunikira kwambiri mwa iwo ndi: Quran yolemekezeka, buku limeneli ndi lozizwitsa zedi ndipo lakhala likudabwitsa mibado pambuyo pa mibado chifukwa cha nfundo za pamwamba zomwe zimagwedeza nzeru za anthu.
Chinanso chimene chimasonyeza za utumiki wake (SAW) ndi mbiri ya khalidwe lake yomwe adamusimba nayo adani ake asanamusimbe nayo omukonda ake, moti ankamutcha kuti “wonena zoona wokhulupirika”.
Umboni winanso ndi zozizwitsa zomwe aliyense amazidziwa zomwe anthu a nthawi yake adaziona, ndipo mibado ya m’mbuyo idamva kuchokera ku mibado ya kale.
Umboninso wina ndi malamulo ogwira mtima, ogwirana bwino, okoma komanso okwanira omwe ali mu chipembedzo cha chisilamu.
Umboni wina ndi nkhani zabwino zolosera za kubwera kwa iyezochuluka zomwe zikupezeka mmabuku akale.
Enanso mwa maumboniwa ndi kufalikira kosalekeza kwa chipembedzo cha chisilamu kumeneku pa malo aliwonse ndi nthawi zonse.
Ndipo umboni wina ndikufotokoza kwake mtumikiyu zokhudza mibado yakale ndi zinthu za mtsogolo (158).

KODI ZINATHEKA BWANJI MTUMIKI KUYENDETSEDWA KUPITA KU JERUSALEM NAKAKWEZEDWA KUPITA KUMWAMBA MPAKA KUBWERERA USIKU umodzi WOMWEWO?

Ndithu mtumiki (SAW) anayendesedwa kuchokera ku makkah kukafika ku mzikiti wa ku Jerusalem pa Buraq (chinyama chokwera), kenako anakakwezedwa kupita ku mwamba motsogozedwa ndi Jibril (Gabriel), ndipo Mulungu ndi wakutha chilichonse, palibe chomwe chingamukanike pansi pano ngakhalenso kumwamba, monga mmene tikuonera lero: amakwanitsa bwanji munthu wofooka kugwiritsa ntchito nzeru zake kupanga ndege yoyenda mwachangu kuposa mau, komanso anapanga chipangizo chojambulira zithunzizomwe zimampangitsa munthu kumaoneka wochuluka ndi malo angapo nthawi imodzi, ndiye Mulungu ndi wamkulu kwambiri yemwe ali ndi kuthekera kwakukulu kuposa zolengedwa zake.

Kodi nchifukwa ninji Muhammad anali mneneri womaliza?

Ndithu kutumizidwa kwa aneneri kumalumikizana ndi cholinga- kumene kuli kuongola ndi kuongolera- ndipo kukupezeka kuti mabuku akale anakumana ndi kusintha ndi kupunguka (ma chapter ndi ma verse ena) pambuyo pomwalira atumiki awo. Mulungu anachiona kuti ndi chanzeru zakuya kuti atumize mneneri ndi buku lomwe silingakumane ndi m’pungwepungwe ngati umenewu (kusintha ndi kupunguka), ndipo Mulungu anatenga udindo woliteteza kufikira tsiku lomaliza, ndipo poona kudabwitsa kwa Qur’an koti ilo ndi buku lomveka bwino lokhala ndi maumboni opambana pa zolengedwa zonse- mpaka kale kale, chinali chanzeru kuti mtumiki Muhammad (saw) akhale womaliza mwa aneneri ndi atumiki.

Kodi nchifukwa chiyani kuli koyenera kuti tizimukonda mtumiki (saw)?

Chifukwa chakuti kumukonda iye ndi imodzi mwa nsanamira zachikhulupiliro, ndipo kukhulupilira mwa Mulungu sikungakhale kokwanira pokha pokha chikondi ichi chitapezeka, ndipo kumukonda Mulungu kumalumikizana ndi kumukonda onse kuti agwire ntchito yaikulu kwambiri ya utumiki imeneyi, chifukwa Mulungu anasankha munthu yemwe ali ndi khalidwe, mau ndi ntchito zabwino kwambiri komanso wochokera ku banja labwino kwambiri, chifukwa iye (Allah) ndi amene amamudziwa bwino munthu woyenera kumpatsa utumiki umenewu, ndipo poona kuti Mulungu ndi amene adamusankha iye pakati pa anthu onse pompatsa udindo waukulu umeneu.
Ndithu ndizoyenera kwa ife kumukonda kwambiri iyeyo kuposa munthu wina aliyense; chifukwa iye ndi amene anawadziwitsa za mbuye wawo, ndipo anali mneneri wabwino kwambiri kwa anthu ake, palibe mwazolengedwa ndi m’modzi yemwe amene anatipangira zabwino zapamwamba woposa iye (saw) (159), iye adapilira ndi mazunzo omwe amapezana nawo pa nthawi yoitanira anthu kuchipembedzo ndi ubwino, moti amabanika ndi kudandaula akamapanda kukhulupilira yemwe iye akumuitanirayo; chifukwa chowadandaulira zokalowa kumoto, Mulungu akunena kuti: “Mwina uziononga wekha pakuwadandaulira (anthuwo) chikhalidwe chawo kuti sakukhulupilira nkhani iyi,(Iyayi usakhale wodandaula ndi zimenezo)” (Surat Al kahaf: 6). Pachifukwa chimenechi mtumiki (saw) ndi amene ali woyenera kumukondetsetsa pambuyo pa Mulungu.

Back to top button