MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPILIRA CHIKHONZERO CHA MULUNGU

Kodi chigamulo ndi chikonzero cha Mulungu ndi chiyani?

Zonzse ziwirizo ndi imodzi mwa msanamira za chikhulupiliro Mulungu akunena kuti: “Ndipo adalenga chilichonse ndikuchilinga mulingo wake” (Surat Al Furuqan: 2) ndipo tanthauzo lachigamulo ndi chikonzero ndiko kuti Mulungu m’mene anadziwa  mmene zinthu zidzakhalire mtsogolo monse zisanapezeke zinthuzo, kapena kulembedwa asadafune kuzilemba komanso asanazilenge(*).

(*)-  Al imanu bil qadhaa wal qadar, Dr. Muhammad Al hamd, tsamba: 36.

KodiMulungu amadziwabwanjizinthu zomwe zidzachitike zisanachitike?

Nzotheka kumuuza chitsanzo chokhuzika komanso chophweka choti: yemwe anapanga masewero (ma game) omwe iye amasewera, amadziwa zomwe gemuyo ingathe kuchita zisanachitike; chifukwa iye ndi amene anaipanga naiikira chilichonse chachikulu ndi chaching’ono chammenemo ntchito yake yomwechizigwira.Ndipo iye amazindikira kotheratu kuthekera kwa gemu imeneyi ndi mbali zomwe izitha kuyambira kapena kugwedezeka ikamagwira ntchito. Ndiye Mulungu ndi amene anamulenga munthu ameneyu yemwe akutha kupanga ma gemu amenewa, choncho Mulungu ndi amene ali ndi kuthekera ndi kuzindikira koposa komanso ndi amene ali wokhonza mokwanira, ndipo iye anachizindikira kotheratu chilengedwe chilichonse asanachilenge, pamene amalenga, ndi pambuyo pochilenga. Ndipo Mulungu ndi amene analenga munthu, nyengo ndi malo, komanso iye amadziwa zomwe zinalipo kale, zomwe zikupezeka nthawi ino, ndi zomwe zidzachitike ntsogolo zisanachitike.

KODI IFE TIMAKAKAMIZIDWA KUCHITA ntCHITO ZATHU KAPENA TILI NDI UFULU WOSANKHA ZOCHITA?

Ndithu munthu amakakamizidwa pa zinthu zina, tonsefe timakakamizidwa ndipo tilibe kusankha pa zinthu monga: kubeleka, kufa, nyengo yokhala moyo, sitimadzisankhiranso makolo, timakakamizidwanso kulumikiza ubale (kusadula ubale). Ngakhale zili choncho komabe tinapatsidwa kusankha pazinthu zina monga; kupemphera kapena kusapemphera (kuswali kapena ayi), kukhulupilira kapena kusankhulupilira ngakhalenso kusankhako kuli choncho; ndithu chifuniro chathu chimakhala mkati mwa chifuniro cha Mulungu; izi zikutanthauza kuti Mulungu akanafuna kuti asatipatse ufulu wosankha akanatha kutero, ndipo akanafuna kutiletsa kapena kukana akanatha kutero. Koma iye anapereka ufulu wosankha kwa munthu kenako akamuwerengere pachisankho chakecho, ilo ndi tanthauzo la Mulungu lonena kuti: “ Ndipo simungafune chithu mwainu nokha pokha pokha atafuna Mulungu mbuye wa zolengedwa zonse” (Surat Attakweer: 29) ndipo tithe kumulongosolera mwanayo tanthauzo la kukakamizidwa ndi kusankha kumeneku, kudzera mu zichitochito, mwachitsanzo mphunzitsi abweretse kapu ya galasi (tambula) ndiye amufunse mwanayo kuti: kodi ungathe kuiponya tambula imeneyi pansi kuti isweke? Zachidziwikireni kuti mwana azayankha kuti: inde ndingakwanitse, kenako mphunzitsiyo amupatse mwanayo tambulayo kuti aiswe, apa mwana uja sadzafuna kuphwanya tambulayo, ndipo mphunzitsi azailandire tambulayo kuchokera kwa mwanayo namufunsa iye kuti chifukwa chiyani sunaiswe tambulayi? Iye adzati kuphwanya tambulayo n’kulakwitsa, sizoyenera kuchita zimenezo,apa mphunzitsi avomereze ndi kuonjezera mau ponena kuti: ndithu Mulungu anadziwa kale kuti iwe sungadzaiswe tambula imeneyi, chifukwa ndiwe mwana wabwino, anadziwanso kale kuti mwana woipa adzaiswa.

Nanga iweyo alipo amene wakuletsa kuiponya tambula imeneyi pansi, kapena pali yemwe akanamukakamiza mwana woipa kuti aiswe tambulayi? M’menemo ndi m’mene chimakhalira chiongoko ndi kusochera. Kenako auzidwe mwanayo kuti: ndithu munthu sadziwa zomwe Mulungu adamulengera, iwenso supemphedwa kuti udziwe zomwe adakulembera, chomwe ukupemphedwa kuchita ndi kukhulupilira kuti kuzindikira kwa Mulungu ndikokwanira ndipo kulibe malire.

Chimodzi modzi kulembedwa kwa zikhonzero: iwe umangofusidwa zachifuniro chako ndi mulingo wako wakutsatira kwako malamulo ndikusiya kwako zoletsedwa, izi zimakhala zochokera mukuthekera kwako ndi chifuniro chako(*).

(*)- Al as-ilatu al aqaidiyyah in-dal atwifali wal ijabatu alaiha, Dr Bassam Al amoosh, tsamba: 145.

Kodi chifukwa chiyani Mulungu adawaongola anthu ena pomwe enasadawaongole?

Mulungu adaongola anthu onse, potengera mau a Mulungu onena kuti: “Ndipo tamulongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoyipa, ndipo tampatsa mpamvu yosankhira njira yomwe akafuna)” (Surat Al Balad: 10),ndipo tanthauzo lachiongoko lomwelili muvesili ndi chiongoko chomufotokozera munthu momveka njira yolungama kuti choonadi chikhale choonekera, komanso bodza lionekere poyera kuti ndi bodza. Mulungu adawasiyira anthu ufulu wosankha, ena amasankha njira yabwino (yoona) pomwe ena amasankha njira yoipa(*).

(*) Al as-iltu al aqaidiyyah in-dal atwifal wal ijabatu alaiha, Dr Bassam Al amoosh, tsamba: 156.

Kodi ngati Mulungu adalemba kale kuti ena mwa ife tizidzalakwitsa ndikusochera, nanga nchifukwa chiyani adzatilange?

Kudziwa uku ndi kwa Mulungu yekha, munthu sadziwa zimenezi,munthu amangoganizira mwaumbuli. Choncho; munthu adzawerengedwa pa ntchito zomwe wagwira pa umoyo wadziko lapansi pano. Ndipo kapolo wa Mulungu sangakwanitse kudziwa zobisika zomwe Mulungu adamulengera iye mpaka atachichita kapena kumupeza. Ndiye chikonzero chomwe chinalembedwa ndi umboni wa chomwe chachitika osati wa chomwe sichinachitike ayi.

Komanso afunsidwe mwanayo kuti: ndithu Mulungu adakulembera zinthu za dziko la pansi… nanga nchifukwa ninji iwe umapanga zokhazo zimene zingakuthandize ndikumasiya zomwe zingakupatse mavuto? Tingathenso kumpatsa chitsanzo choti: munthu atafuna kupita dziko lina lake lomwe lili ndi njira ziwiri; imodzi mwa njirazi ndiyosaopsa pomwe inayi ili ndi chiopsezo, kodi munthu angasankhe njira yanji pa njira ziwirizi? Mosakaikitsa iye adzasankha njira yosaopsayi, chimodzimodzinso popita ku umoyo womwe uli nkudza munthu amasankha njira yachitetezo kuti akafike ku Jannah – njira imeneyi ndiyo kutsatira malamulo ndi kusiya zoletsedwa- , zikadakhala kuti chikonzero ndi umboni wa aliyense, sitikadakwanitsa kuwagwira olakwa ( criminals), chifukwa iwo akadapereka umboni woti iwo achita zimenezi chifukwa cha chikonzero[*], choncho munthu akuyenera kusangalatsidwa ndi chikonzero ndikuzisiya mmanja mwa Mulungu wapamwambamwamba , chifukwa Mulungu“ Safunsidwa pazimene akuchita koma iwo (anthuwo adzafunsidwa” ( Surat Al-Anibiyay:23), zolengedwa zonse ndi zake ndipo malamulo onse ndi ake ndipo iye ndi mwini kulamula.

*  Al iman bil qadhaa wal qadar, Dr Muhammad Al hamd, tsamba: 130- 134.

Why Did Allah Create Us? What is the Origin of the Universe? Why Did Allah Create Animals?

Allah said: “And I did not create the jinn and mankind except to worship Me Alone.” Allah created us for a purpose that benefits us which is worshipping Him. The outcome for fulfilling or neglecting this purpose is Paradise or Hellfire, respectively. Allah masterfully created the universe with its skies, land, planets, and stars that are signs of His greatness. He made the sun provide us with warmth to help nurture plants and to kill germs. He made animals available to humans so we can eat them or carry our belongings on them. He said: “And [He created] the horses, mules and donkeys for you to ride and an adornment. And He creates what you do not know.”

Kodi chifukwa chiyani Mulungu anatilenga? Nanga zolengedwa zinayambika bwanji? Nanga ndi chifukwa chiyani Mulungu analenganso zinyama?

Mulungu akunena kuti: “Sindidalenge ziwanda ndi anthu koma kuti azindipembedza” (Surat Adhariat: 56), ndithu Mulungu adatilenga ndicholinga chopindulira ife tomwe- kumupembedza iye-, ndipo anayika zotsatira zake kuti lidzakhale tsiku lomaliza molingana ndi ntchito zathu, Jannah kwa olungama ndipo moto kwa ochimwa. Ndipo dziko lonseli (الكون) ndi cholengedwa cha Mulungu, ilo linalengedwa mwaluso ndi mwanzeru zakuya, analenga mitambo ndi nthaka, anaikamonso m’menemo maiko (planets), analenganso nyenyezi, kukhala zizindikiro, phunziro, ndi zikongoletso zadzikoli, ndipo analenga dzuwa kuti lidzitipatsa kutentha, kuotcha komanso kuthandizira kumeretsa mbeu ndi kupha tizilombo toyambitsa matenda (germs), ndipo adalenga zinyama kuti zitumikire anthu, azizidya, kuzikwera kapena kunyamulira katundu wawo, Mulungu akunena kuti:“Adalenganso ngamila, nyumbu ndi abulu kuti muzizikwera ndikutinso zizikhala zolowetsa chisangalalo mmitima yanu ndipo adzalenga zokwera zina mtsogolo muno zomwe simukuzidziwa”(surat Annahal: 8), ndiye kulenga nthaka ndi zinthu zimenezi kunachitika munthu asanalengedwe, konseko ndikumulemekeza munthuyo mwapadera dera kuposa zolengedwa zina- ngakhale zolengedwa zina zonsezo zimamutamanda Mulngu, izonso pazokha zimapembedza Mulungu, Mulungu akunena kuti: “Ndipo palibe chilichonse (mwa zolengedwa) koma chikulemekeza ndi kutamanda Mulungu koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo ndithu iye Mulungu ngodekha, ngokhululuka” (Surat Al Isra:44)[*].

*  Al hikmatu min khalqi al hayawan wannabat qablal insan, markaz al fatwaa, islam web, 18/5/2006.

Kodi Mulungu adzawawerengeranso anthu omwe sadawapeze mtumiki aliyense?

Iwo adzakakhala pakati pa kufunsidwa ndi kuwerengeredwa, chifukwa Mulungu adawapatsa iwo nzeru, ndiye Mulungu adzawayesa mayesero pa tsiku lachiweruziro ndikuwalamula, akadzayankha molondola ndikumvera akalowa ku Jannah, koma akadzanyozera adzalowa ku moto.

Kodichifukwachiyanikunapezekanso zoipa?

Dziko limeneli ndi malo a mayesero ndipo lili ngati gawo loyamba la nkhani yamagawo awiri, pomwe moyo uli nkudza ndi malo amalipiro ndikuwerengeredwa komanso kubweza opondereza zomwe adawapondereza oponderezedwa, ndipo tsiku lomalizali lili ngati gawo lachiwiri la nkhani ija, pachifukwa chimenechi ndithu kupezeka kwa anthu oipa ndikusawalanga kwawo pa dziko la pansi pano, amenewo ndi mayesero ndipo pa (moyo wa dziko lino ) umenewu  simathero a zonse ayi, koma padzafunika kuuka kwa akufa tsiku lachiweruziro kuti aliyense akapeze malipiro antchito zake, Mulungu akunena kuti: “Choncho amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono adzaona malipiro ake, ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono adzaona malipiro ake”. (Az-zilzaal: 7-8)[*].

* Alqawaidu al’ashri ahamul qawaid fii tarbiati al abunai, Dr. Abdulkareem Bikar, tsamba: 21- 22.

Kodi chifukwa chiyani Mulungu adalenganso anthu oipa?

Ndithu Mulungu adalenga anthu ndikuwapatsa ufulu wosankha zabwino kapena zoipa. Iweyo ungathe kukhala wakhalidwe labwino kapena loipa, koma umayenera kuzilandira zotsatira zakhalidwe lako ndipo uwu ndi mtendere ndi nzeru zakuya zochokera kwa Mulungu; moti anthu oipa aja angakwanitse kukhala abwino,ndipo ntchito yathu ndi kuwathandizira chimenechi, akakana napitiliza kuipa, kudzakhala koyenera kwa ife kuwaletsa kuchitira zoipazo anthu ena , ndicholinga choti Mulungu atikonde ndikutilipira, ndipo Mulungu ndi amene analenga chilichonse mu umoyo uno, ndipo moyo uno ndi malo amayesero, Mulungu akunena kuti: “ Amene walenga infa ndi moyo kuti akuyeseni mayeso ndani mwainu ali wochita zabwino kwambiri” (Suratul-mulk:2), ndipo ena mwa mayesero amenewa ndi kupezeka kwa zoipa mmanja mwa satana ndi anthu osochera[*] [*]  Al Asiilatu al aqaidiyyah in-dal atfaali wal-ijabatu alaiha, Dr. Bassaam Al ‘amoosh, tsamba: 155

Kodi chifukwa ninji allah adalenga anthu ena kukhala olumala kapena a zilema?

Iwo amakhala kuti Mulungu awayesa mayeso owapungula china  chake kapena powapatsa matenda; ndi cholinga choti akapirira Mulungu akawaonjezere zabwino, komanso ndicholinga choti amene ali abwino  athokoze mtendere womwe Mulungu wawapatsa powapanga ambiri mwa iwo kukhala alungalunga (opanda chilema) ndi athanzi (opanda matenda), kuti tizimuthokoza pa zimenezi, komanso ndicholinga chotikumbutsa kuchepera kwa kuthekera kwathu poyerekeza ndi kuthekera kwa Mulungu, kotero palibe chifukwa chodzitukumulira, koma tizidzichepetsa ndi kuthandizana wina ndi mzake, ndipopa tsiku lowerengetsera: anthu opanga zabwino akakhala moyo wosatha ali athanzi (osadwala) mminda ya mtendere – mu chifuniro cha Mulungu[*].

[*] Rudoodun ala shubuhatin muta’addidah, markaz alfatwa, islam web 7/6/2007.

Kodi chifukwa chiyani kuli ena olemera ndi ovutika? Nanga chifukwa chiyani oipa ena amakhala mu nyumba za pa mwamba kwambiri (palace) pomwe olungama ena akukhala mmasakasa?

Ndithu chuma chonse cha padziko lapansi chinachokera kwa Mulungu, ndipo Mulungu amawayesa akapolo ake, nthawi zina amawapatsa chuma anthu abwino kuti awayese ngati azithandiza anthu ena, ndipo nthawi zina amamumana chuma kuti amuyese m’mene angamapililire osaba kapena osapanga nsanje, ndiye nthawi zonse zomwe  munthu wabwino ameneyu angakhale mu umoyo  wochepaumenewu (wadziko lapansi) ali wopilira ikamupangitsa kupeza malipiro akulu kwambiri tsiku lowerengetsedwa, pomwe yemwe anapatsidwa chuma chambiri ndipo sanathandize anthu ena nazunza nacho anthu ena, adzakalangidwa tsiku louka kwa akufa; chifukwa iye sanathokoze mtendere wa Mulngu.

Tingathenso kumuuza kuti: ndithu Mulungu analenga anthu m’magulu osiyana siyana olemera ndi osauka; ndicholinga choti olemera achitire chifundo osauka, ndipo amphamvu athandize ofooka, Mulungu ali ndi cholinga chapamwamba powasiyanitsa anthu pa chili chonse, zilankhulo zawo ndi zosiyana siyana chimodzimodzinso mitundu yawo, mafuko ndi zibadwa zawo ndi zosiyana, ena ndi otakataka pomwe ena ndi aulesi ena amatha kutengera za anzawo pomwe ena ndiofuna zawo zokha, ena opereka ndipo ena ndi aumbombo, amasiyananso pachuma ndi zinthu zina zomwe ali nazo, ena ndi olemera ndipo ena ndi osauka, koma onsewo ndi mayesero, kulemera ndi mayesero ndipo kusaukanso ndi mayesero; amamuyesa wolemera kuti kodi athandiza anthu ena? Adzapereka chopereka chapa chaka (zakah)? Adzapereka chopereka chaulere chanthawi ina iliyonse (sadaka)? Ndipo amamuyesa wosauka kuti kodi apilira? alimbikira kugwira ntchito? Aziyenda yenda dziko lapansi kufuna funa chuma (mariziq)? Kapena azipanga ziphuphu (katangale)? Kapena azikhalira kuba?

Onsewa ndi mayesero, koma chitsimikizo chokalowa kumtendere chili pa onse; ndithu chuma chimachokera kwa Mulungu, ndipo kulemera ndi kusauka sikumalepheretsa kukalowa ku Jannah kapena kumoto, ndipo aliyense amalamulidwa molingana ndizomwe ali nazo ndipo anthu onse anakakhala olemera, sakanapezeka womugwilira ntchito nzake, ndipo palibe yemwe akanafuna thandizo kuchokera kwa nzake, Mulungu akunena kuti:“ Ndicholinga choti ena mwaiwo awachite anzawo kukhala antchito awo”(surat Azuhulf: 32), kutanthauza kuti aziwalirana( azitumikira ena kwa anzawo) wina ndi nzake, umu ndi mmene theyara la moyo uno limayendera koma kuti anthu onse akhale ofanana, ndiye kuti umoyo utha kuima[*].

* Al Murabbuna watasaa-ulaatil-atfaali, Nuwaalu Al Khalifah, tsamba: 96.

Kodi chifukwa chiyani timadwala? Nanga chifukwa chiyani munthu amakumananso ndi mavuto?

Mulungu amakhala akumuyesa munthu wina aliyense kuti kodi apilira kapena akwiya? Ndipo Mulungu amamulipira munthu wopilira malipiro aakulu zedi, munthu wokhulupilira adzasangalala ndi malipiro amenewa patsiku louka kwa akufa, ndiye matenda, mavuto ndi zowawa, zonsezo ndi zikonzero zomwe Mulungu adayika kuti akwezere masitepe a anthu ndikuyeretsera mitima ndi zikhalidwe zathu kuti tisakhale odzimva ndi odzikweza, ndipo m’menemo ndimomwe wokhulupilira amadziyandikitsira kwa mbuye wake pomupempha komanso popilira,ndipo chikhulupiliro chake ndi zabwino zake zimaonjezereka,komanso Mulungu amamukonda, komanso (amatiyesa) kuti munthu aphunzire kufunika kwa thanzi ndi mitendere ina yomwe Mulungu amatipatsa.

Tingathenso kumupatsa chitsanzo cha galimoto, timufunsa iye kuti: kodi chifukwa chiyani idapangidwa galimoto? Kuti iziyenda, si choncho? Nanga nchifukwa chiyani kampani imene idapanga galimoto imeneyi inayika mu galimotomo ma bureki? Kodi zimenezi sizimatsutsana ndi kuyenda kwakeko? Ndithu kugwiritsa ntchito ma bureki ndi kofunikira ndi cholinga chofuna kusamala galimotoyo, galimoto inapangidwa kuti iziyenda pomwe ma bureki kuti iziima (isamayende) pa nthawi yoyenera kuti isamuvulaze mwiniwakeyo, ngakhale Mulungu anatilenga kuti tizisangalala popembedza iye komanso tizisangalala ndi mitendere yomwe iye anatipatsa.

Komabe analenganso mavuto kuti azimukumbutsa munthu wa chibwana komanso wotailira chintchito chake chachikulu chomwe Mulungu adamulengera,kotero asiye kutailira ndi kuiwala kwakeko, ayambe kumukumbukira Mulungu pomupempha chikhululuko, kupirira ndikukhala ndi chiyembekezo mwa Mulungu[*].

*  Al-imanu bil qadhai wal qadar, Dr. Muhammad Al hamud, tsamba: 152-160.

Kodi Mulungu ndi amene adalenga zinyama ndi tizirombo tozunzati?

Mulungu ndi mlengi komanso mbuye wa chili chonse , Mulungu adalenga izo mukuthekera kwake komanso ndi cholinga cha nzeru za pamwamba; chifukwa Mulungu ndi wanzeru zakuya komanso ndi wozindikira, amadziwa zokhudza zinyama zimenezi zomwe ife sitidziwa; chifukwa kudziwa ndi kuzindikira kwathu komwe Mulungu anatipatsa ndi kwapang’ono zedi poyerekeza ndi kudziwa komanso kuzindikira kwa Mulungu, pa chifukwa chimenechi Mulungu akunena kuti: “Ndipo inu simunapatsidwe nzeru (zozindikira zinthu) koma pang’ono chabe”. (surat Israai: 85),ndiye ife sitingathe kudziwa zolinga zonse zomwe Mulungu analengera zinyama zimenezi,komabe zina mwa zolinga zimenezi ndi: kuonetsa ukadaulo wa Mulungu pa zolengedwa zake ndi kayendetsedwe kake ka zolengedwa zake,ngakhale zachulukitsitsa iye amazidyetsa zonsezo, chimodzimodzinso amatiyesera nazo mayesero ndikumulipira yemwe wazunzidwa ndi zinyama zimenezi, komanso zimaonetsa mphamvu zayemwe wapha zinyama zimenezi, ndipo zimaonetsa kufooka kwa munthu akamazunzika ndikudwala chifukwa cha cholengedwa chomwe ndi chaching’ono kwambiri poyerekeza ndi munthu. Ndipo kudzera muzachipatala ndi kafukufuku zapezeka kuti mankhwala ena amachokera ku poison wanjoka ndi zina zotero, komanso njoka zimadya mbewa (makoswe) zomwe zimaononga mbewu zakumunda, ndipo zina mwa zilombo zozunza zimenezi ndichakudya cha zinyam zina zaphindu, izi zikupanga tcheni (life cycle) cha moyo wa zolengedwa chomwe Mulungu adachilenga mwaukadaulo[*].

* As-ilatu twiflika al harijah, Abu Majdi Harak, tsamba: 31.

Kodi chifukwa chiyani ndimakakamizidwa kupemphera kasanu pa tsiku?

Ndithu mapemphero omwe Mulungu anatikakamiza ali ngati njira zoyeretsera mtima wa munthu ndi kutukulira mzimu wake kukhala wapamwamba. Licheperenji thukuta lomwe limakhetsedwa pochita mapempheroamenewa, poyerekeza ndi zabwino zomwe amapeza akatero[*]. Ndiye pachifukwa chakuti mumapemphero (swalat) muli kuwerengedwa kwa Qur’an, kumutchula Mulungu (dhikiri) ndikumupempha Mulungu (dua), amasokhanitsa mapemphero amenewa (swalayi) mitundu yosiyana siyana ya mapemphero (ibadah) mokwanira, izizikupangitsa mapephero (swalat) kukhala opambana kuposa kuwerenga Quru’an pa kokha, ndikutchula Mulungu (dhikiri) pa kokha, komanso kumupempha Mulungu(dua) pa kokha. Zilichoncho chifukwa swalat imasonkhanitsa zonsezo kuonjezeranso pamapemphero a ziwalo[**] .

Ndithu anthu okhulupilira amasangalatsidwa ndi swala chifukwa iwo mu swalamo amakhala chifupi komanso akulankhulitsana ndi Mulungu, akumupempha zonse zomwe amazilaka laka, ndipo Mulungu ndikumayankha; ndipo ife timapemphera (swalah) chifukwa chakuti Mulungu anatilamulira kutero, ndipo ife nthawi zonse timafuna kumapanga zomwe Mulungu watilamula, ndipo timagwadira Mulungu chifukwa iye ndi amene anatilenga ndipo iye amatidyetsa, ndipo iye ndiye woyenera kupembedzedwa pachifukwa cha mitendere yosawerengeka yomwe watipatsa, Mulungu akunena kuti: “ Ngakhale mutawerengetsera mtendere wa Mulungu simungakwanitse kuwerengetsera yonse” (surat AN-nahali: 18), ndithu kupembedza kumeneku kuli ngati kuonetsa chikondi chathu ndikuthokoza kwathu kwa Mulungu, komanso kuonetsa kuti ife timafunikira thandizo la Mulungu, ndicholinga choti atisungire thanzi lathu ndi kutipatsa kuthekera kopanga zabwino ndikutichingira zoipa, pomwe Mulungu safunikira zimenezo, chifukwa iye ndi wolemera kwambiri safuna thandizo lathu ngakhale la ntchito yathu ndipo sizingamuthandize kathu.

Ndiye mapemphero ndi malamulo ochokera kwa Mulungu omwe iye anafuna kuti tizimupembedzera kudzera munjira yomwe anabweretsa mtumiki Muhammad (saw), ndipo ilo ndilo tanthauzo la maumboni awiri (shahadatain), kutanthauza kuti timamupembedza kudzera muchiphunzitso cha mneneri Muhammad, choncho chifukwa chakuti mapemphero amenewa ndi njira yathu yopezera malipiro aakulu omwe akatipangitse kukalowa ku Jannah, ndithu Mulungu anali ndicholinga cha pamwamba choti asakamupatse munthu wina aliyense malipiro pokha pokha agwire kaye ntchito, pachifukwa chimenechi, Jannah ndi katundu (malonda) wa Mulungu,- ndipo ngodula zedi-, kotero akufunikira kukhala ndi mtengo waukulu womwe uli kumvera (malamulo aMulungu)[***].

*Al-imanu wal hayatu, Dr. Yusuf Al Qardhaawiy, tsamba: 6.
** Al waabil asswayyib, Ibun Al Qayyim, tsamba: 234.
*** As-ilatu twiflika al harijah, Abu Majdi Harak, tsamba: 32

Ndakhala ndikupempha pa mapemphero (swalah) yanga kuti ndikule mwa changu koma Mulungu sanandiyankhe?

Ndithu pempho (dua) lili ndi miyambo yake yofunika kuitsatira ina mwaiyo ndi: wopempha alemekeze malamulo ndi chiphunzitso cha mtumiki pa dua kapena malamulo omwe Mulungu adaika oyendetsera dzikoli, ife timamupempha Mulugnu ndipo iye amatipangira zabwino kwambiri zomwe amatisankhira, nthawi zina umatha kuwapempha bambo ako kuti ukaseweretse njinga pa msewu wamagalimoto iwo ndi kukana; chifukwa iwo amakukonda kwambiri ndipo aona kuti kusakuvomera pempho lako ndizomwe zili zabwino kwambiri kwa iwe, ndiye malinga ndi kuolowa manja kwa Mulugu amaiika dua yathu pa imodzi mwanyengo zitatu: yoyamba: atha kutiyankha ndi kutitheketsera zomwe tapemphazo, yachiwiri: atha kutichotsera nayo (duayo) vuto kapena choipa china chake chomwe chikanatigwera, yachitatu: atha kutisungira chomwe tapemphacho kuti tikachipeze kapena chikatichitikire ku Jannah tsiku louka kwa akufa chinthu chabwino kwambiri kuposa chomwe tinapemphacho[*].

*  as-ilatu twiflika al harija, Abu Al majd Harak, tsamba: 35.

KODI CHIFUKWA CHIYANI INE SINDILI WOKONGOLA NGATI NZANGA UJA?

Chifukwa Mulungu adamulenga munthu wina aliyense m’maonekedwe osiyana ndi nzake, ndipo cholengedwa ndi Mulungu chili chonse ndi chokongola monga mmene Mulungu akunenera kuti “Palibe chikaiko, tamulenga munthu m’kalengedwe kabwino (kwambiri)” (surat tini: 4), ndiye munthu wina aliyense amadziwika potengera kalengedwe kake, moti yemwe Mulungu adamulenga kukhala wokongola kwambiri akuyenera kuthokoza kwambiri, ndipo yemwe Sali choncho akuyenera kusangalatsidwa nazo ndikuchilandila chimenechi, ndipo yemwe angathokonze ndiyemwe angapilire ali ndi ma sitepe ndi malipiro akulu zedi[*].

*  Almurabboon watasaa-ulaati al-atfaal, Nuwalu Al Khalifah, tsamba: 95.

Ngati Mulungu amatikonda nanga nchifukwa chiyani zimatichitikira zoipa?

Ndithu Mulunguamatiyesa ndi cholinga choti asiyanitse pakati paanthuolungama ndi anthu oipitsa, Mulungu amatha kumuyesa munthu ndicholingachoti munthuyo azithawira kwa iye, ndi kudziyandikitsa kwa iye nthawi zonse, ndiye mayesero omwe Mulungu amawayesa nawo okondedwa ake, amakhala ndi cholinga chowaonetsera poyera kuti iwo amawakonda, ndi kuwakwezera ma sitepe awo ndikuti akhale chitsanzo cha ena; kuti nawonso azipilira ndikukhala ngati iwo, pachifukwa ichi mtumiki (saw) anati: “Anthu omwe amayesedwa mayesero kwambiri ndi atumiki kenako anthu olungama kwambiri kenako otsatira paiwo (pakulungama)” (Bukhar: -992), ndiye munthu amayesedwa molingana ndi sitepe yake (yomwe ali) pachipembedzo, akakhala wolimba pachipembedzo, Mulungu amamukhwimitsira mayesero, ichi ndi chifukwa chomwe Mulungu amawayesera aneneri maysero akulu kwambiri, ena mwaiwo mpaka anaphedwa, ena kuzunzidwa, ena kudwala kwambiri komanso nthawi yaitali monga: Ayyubu, ndipo mtumiki wathu Muhammad (saw) anazunzidwa ku Makkah ndi ku Madinah, komabe iye anapilira.Mfundo yaikulu pamenepa ndiyakuti mazunzo amabwera pa anthu okhulupilira ndi oopa Mulungu molingana ndikuopa kwawo Mulungu ndi chikhulupiliro chawo[*], ndipo zikuyenera kukhazikika mu mtima mwa mwana kuti: ndithu Mulungu amapanga zomwe wafuna, ndipo Mulungu safunsidwa pazochita zake, chifukwa iye ndi wolamula kuposa olamula onse.

* Kaifa taqooluha li-atfaalika; Paul Cool Man, p/156.

Back to top button