MAU OYAMBA

Ndithu kutamandidwa konse ndi kwa Allah bwana wazolengwedwa zonse, ndipo madalitso ndi mtendere zipite kwa wolemekezeka wa aneneri onse wa pamwamba ndi wopambana wa atumiki onse, mneneri wathu Muhammad, ndi omutsatira onse.

Pambuyo pa kutero:-
Nditthu zaka zoyambilira za umwana zili ndi ubwino wa ukulu pokonza m’mene mwana azionera chilengedwe, chifukwa chithunzi thunzi chomwe chimadzalidwa mu nzeru za mwana mu nyengo imeneyi, chimatengedwa ngati mwala wa maziko womwe umakonza umunthu wa mwanayo kumbali zake zonse (zosiyana siyana) ndipo umafunikira (mwalawo) kuti uziyendera limodzi ndi zofunikira za mwanayo zokhudza umoyo, chikhalidwe ndi chipembedzo, zomwe zingamuthandize mwanayo kuti ayambe mwa mphamvu ulendo wake wolowa mu zipsinjo ndi mikwingwirima ya umoyo (mavuto) ndi kudutsamo molongosoka ali munthu waphindu komanso wothandiza kudzera mu zimene akumazimva ndi kuziona, amakonzanso chitsanzo chake chake chadzikoli, kotsala kwa moyo wakeko pambuyo pa zimenezi kumangokhala kukonza kapena kupititsa patsogolo chithunzi thunzi chake choyambilira chija potengera nyengo zimene akudutsana nazo.

Mu nyengo imeneyi mwana amadalira makolo ake ngati njira yodziwira zinthu, chifukwa kulongosoka kwa ana kumachokera mu kulongosoka kwa chikhalidwe cha makolo, iwo ndi amene ali ndi udindo wophunzitsa ana awo. Pa chifukwa chimenechi, adalankhula mtumiki (saw) kunena kuti “aliyense mwa inu ndi muyang’aniri ndipo aliyense mwa inu ali ndi udindo pa chomwe akuyang’anira” (muslim). Moti chilamulo chimenechi chikukakamiza kuyikira mtima ndi kulimbikira pa maphunziro ndi kuphunzitsa.

Poona kuti ife tili mu nyengo yomwe yadzadzana ndi zilako lako ndi zisokonezo: kunali kofunikira kwambiri kuti makolo alimbikire kuphunzitsa ana (kulimbikira kwake) kodzadzidwa ndi chilungamo, chidwi komanso kupereka mpata wokwanira (kwa ophunzirawo),chifukwa kutheka njere imene makolo angayidzale mmitima ya ana itha kubala ntchito yopitilira kwa makolo akadzachoka moyo uno (akadzamwalira), nakhala mwana uja ntchito yopitilira ya makolo pambuyo pa ifa ya makolowo (sadaqah jaariyah), ngati m’mene adanenera mtumiki (saw) – pamene amatchula zinthu zomwe zimakhala zikumuthandizabe munthu ngakhale atamwalira – kunena kuti “kapena mwana wabwino yemwe amawapemphera zabwino makolo ake”. (Muslim).

Ana ndi chithu chimodzi mwazithu zomwe Allah anawalangiza makolo (kuti achisamalire), ngati m’mene Allah akunenera mu buku lolemekezeka la Quru’an kuti: “Mulungu akukulangizani zokhudza ana anu” (sura 4 :11)

kutanthauza kuti ndithu ana anu (inu makolo) painu ndi chosungitsidwa, ndipo Allah wakulangizani za iwo kuti muwasamalire chipembedzo chawo ndi dziko lawo, ndipo mudziwaphunzitsa ndi kuwalangiza ndi kuwaletsa zoipa ndi kuwalamulira kuti azimumvera Allah ndi kusamala malamulo ake nthawi zonse, ngati m’mene akunenera Allah mu quruan yolemekezeka kunena kuti “E, inu amene mwakhulupilira! dzitchinjirizeni nokha ndi mawanja anu ku moto…” (sura 28:6).

Allah anawalangiza makolo za ana awo, zili ndi iwo kugwiritsa ntchito langizolo ndi kukapeza Jannah kapena kuliononga ndi kupeza chilango, zimenezi zikusonyeza kuti Allah ndi wachisoni kwambiri kuposa makolo awiri; moti anawalangiza makolo awiri zoyang’anira ana awo mwa ubwino kumachita kuti makolo amakhala achisoni nkale kwa ana awo (1).

Choncho, kuphunzitsa mwana m’banja kukakhala kuti kwachitika mwa ubwino, mwana ameneyo amadzakhala wa chitsanzo cha pamwamba. Ndipo kusowekera kulikonse kwa maphunziro ndi maleledwe a chikhulupiriro cholongosoka mwa mwana m’banjamo, kudzatulutsa mwana wosowa khalidwe labwino (2) .

Sikuti maphunziro ndiye kungokonza zolakwika zokha ayi, koma kuphunzitsa ndi kupereka maziko a chipembezo ndi malamulo a chisilam ndi kugwiritsa ntchito njira zosiyana siyana monga kukhazikitsa zithuzi thuzi (za zomwe ukumuphunzitsa) ndi kuzipangitsa zimenezo kuti zikhazikike mmitima mwawo – monga kuphunzitsa kudzera mukuonera kwa ena, ulaliki, nkhani, zochitika,ndi zina zotero (3) ; ncholinga choti titulutse munthu wolongosoka komanso waphindu pa umoyo komanso pa mudzi ( pa malo).

Bukuli lagawidwa m’magawo awiri : gawo loyamba (zokhudza maphunziro a chikhulupiliro ), m’menemo muli maziko ambiri omwe angathandize makolo kuphunzitsa ana awo – mu chifuniro cha Allah -, pomwe gawo la chiwiri likuzungulira pa (zitsanzo zochitika pakayankhidwe ka mafunso a ana okhudza chikhululupiliro) m’menemo tiyankhamo mafunso amene ali otchuka kwambiri pakati pa ana amisinkhu yosiyana siyana, makamaka omwe akukhudzana ndi msichi zachikhulupiliro zisanu ndi imodzi (6) ndipo tafotokozamo momveka bwino m’mene tingayankhire mafunso ngati amenewa.
Ndithu Allah ndi mwini kuthekera, komanso muwongoli ku njira ya chiongoko.

Abdullah bin Hamd Alrakaf

Back to top button