NSANAMIRA ZA MAPHUNZIRO Aza CHIKHULUPILIRO

Msanamira yoyamba:

Kukhulupilira mwa Mulungu mmodzi yekha

Chibadwa cha munthu, nzeru zake ndi malamulo a Mulungu zimasonyeza kuti Mulungu alipo, moti chilengedwe china chilichonse pachibadwa chake chimakhulupilira za mulengi wake.Ndipo kudzera munzeru; zimavomereza kuti zolengedwa zonsezi alipo amene anazipezeketsa, pomwe kudzera m’malamulo a Mulungu; tikupeza kuti zipembedzo zonse zomwe zinachokera kumwamba zinavomereza kuti kuli mulengi.

Mu kukhulupilira mwa Mulungu muli zinthu zinayi:-
choyamba: kukhulupilira kuti Mulungu alipo.
chachiwiri: kukhulupilira zaumbuye wake, kuti iye ndi mbuye, Mlengi,wopereka, wodyetsa, ndi woyendetsa chili chonse.
chachitatu: Iye yekha ndiye woyenera kupembedzedwa mu umodzi wake ndikuti alibe wofanana naye.
chachinayi: kukhulupilira maina ake ndi mbiri zake zomwe zimatsindika zakukwanira kwake ndi ubwino wak.
Choncho timuphunzitse mwana zinthu zinayi zimenezi kuti akule akumudziwa Mulungu ndi kumukuza ndi kumukonda, nsanamira imeneyi (ya kukhulupirira mwa Mulungu) ndi manthu wa nsanamira zina zotsarazo.

 

CHIFUKWA CHIYANI TIMAWAPHUNZITSA ANA KUKONDA MULUNGU

 1. Chifukwa Allah wolemekezeka ndi amene anatipezeketsa ife, natilenga mkalengedwe kabwino natipanga ife kukhala apamwamba kuposa zolengedwa zina, ndikutipatsa ife mtendere wa pa mwamba kwambirichimene chili chisilamu-, komanso anatipatsa ma ubwino ochuluka osalingana ndi m’mene tilili, pambuyo pake ndikutilonjezanso Jannah; kukhala malipiro antchito zathu zomwe, komanso mphatso yopatsidwa kuchokera kwa Mulungu, iye ndi mwini kupereka maubwino anthawi zonse padziko lino ndi ku umoyo wosatha.
 2. Chifukwa chakuti chikondi chimabweretsa kulemekeza ndi kuopa mwa chinsinsi kapena moonekera, Pali kufunikira kwa kuti ana athu azilemekeza mbuye wawo komanso azimuopa osati azingoopa chilango chake ndi moto ayi, mapemphero awo azikhala chowasangalatsa chawo ndi chowateteza kukusochera.
 3. Chifukwa chakuti Mulungu ndi wamoyo mpaka kale kale yemwe sadzamwalira, yemwe saodzera kapena kugona iye amakhala ndi anthuwo nthawi zonse, komanso iye ndi amene amawateteza iwowo kuposa m’mene amachitira makolo awo, choncho kuyedzamira kwawo mwa Mulungu ndikumukonda kwawo kumatengedwa kuti ndikofunikira kwambiri, kuti adziwe kuti ali ndi chochiyedzamira champhamvu yemwe ndi Mulungu wapamwamba mwamba.
 4. Chifukwa iwo akamukonda Mulungunayikondanso Quru’an, iwo azilimbikira kupemphera.
  Ndipo akadziwa kuti Mulungu ndi wabwino amakondanso zabwino ndiye kuti azipanganso zonse zomwe zili zabwino, ndipo akadziwa kuti Mulungu amakonda anthu olapa kwaiye, oziyeretsa, ochita zabwino, opereka chaulele, opilira, oyedzamira mwa Mulungu, osamala malamulo a Mulungu amalimbikira kuti atchuke ndi mbiri zimenezi, oterowo amafuna kupeza chisangalaro cha Mulungu ndi chikondi chake komanso ubwezi ndi Mulungu, ndikuti Mulunguyo aziwateteza iwo (61).
  Ndipo akadziwa kuti Mulungu sakonda anthu achinyengo, okanira, odzikweza, opsola muyeso, opondereza ndi anthu oyipa; iye amayetsetsa kupewa mbiri zonsezi malinga ndi kuthekera kwake chifukwa chomukonda Mulungu ndi kufuna kumusangalatsa.
 5. Chifukwa kumukonda Mulungu zimatanthauza kuti Mulunguyo alipo, zimenezi zimapangitsa kuti apeze mpumulo, kudekha ndi kukhazikika, ndipo samadandaula kapena kubanika, pakutero amapeza mtendere wa mu mtima ndi thupi kumatenda amaganizo ndi ziwalo, koma chofunikira kwambiri kuposa zimenezi ndiko kutetezeka kumachimo(62).

TINGAWAPHUNZITSE BWANJI ANA ATHU KUKONDA MULUNGU

 1. Njira yokhayo yodzalira chikhulupiliro mwa mwana ndikugwiritsa ntchito njira yokhudzika (sense organs), kutanthauza kuti: ife timadalira ziwalo (sense organs) polimbitsa chikhulupiliro cha mwana pa mbuye wake, moti timagwiritsa ntchito chikhalidwe choonekera chomwe chamuzungulira mwanayo monga: dzuwa, mvula ndi pempho (dua)-, kudzera muzimenezi timamuphunzitsa mwanayo kuti kuli Mlengi yemwe akuyendetsa dziko limeneli ndipo timamulimbikitsa kuti azifunsa zomwe sakudziwa(63),ndipo timayesetsa kuyika chithuzi thuzi chachikhulupiliro m’maso mwa ana kuti azitha kuona maumboni oti Mulungu alipo kuchokera pazomwe akulongosoleledwa ndi kuphunzira pamaphunziro(64).
  Choncho tiyesetse kuwalitsa luso la Mulungu lodabwitsa ndi lapamwamba, monga m’mene Mulungu akutiongolerera kuti tiziona ndikulingalira za chiyambi chakalengedwe kamunthu, Mulungu akunena kuti “Aganizire munthu kuti kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani?” (Surat At Tariq: 5), akunenanso kuti “Ndimwa inu nomwe; kodi simuona (simulingalira)?” (Surat Adhariyat: 21), komanso tizilingalira za chakudya cha munthu kuti Mulungu anachipezeketsa bwanji, ndi kufotokozera ndondomekoyomwe chayenda (steps), Mulungu wapamwamba mwamba akunena kuti “Alingalire munthu (m’mene chilili) chakudya chake” (Surat Abasa: 24), komanso tionetse ukadaulo wa Mulungu pa zolengedwa zakezi zomwe zimasonyeza ukulu wake ngati m’mene Mulungu akunenera kuti “(Kodi akunyozera kulingalira zisonyezo za Mulungu), sakulingalira za ngamila (camel)kuti idalengedwa motani?” Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)?” Ndi mapiri ndi momwe adakhazikitsidwira, Ndi nthaka momwe idayalidwira”. (Surat Al Ghashiyah; 17- 20).Nzotheka kuyandikitsa matanthauzo akulu akulu amenewa ndikudabwitsika kwa chilengedwe ndi ukulu wa Mlengi ndi luso lake (Mulunguyo)munzeru za anawo malinga ndi misinkhu yawo yosiyan siyana pogwirtsa nchito zipangizo zofotokozera momveka, zosiyana siyana zomwe zikupezeka pogwiritsa ntchito luso lamakono (technology)(65), choncho mwana pachibadwa chake adzamukonda aliyense yemwe anamulengela iye zinthu zazikulu zikulu zonsezi ndikumuphunzitsa iyeyo (maphunziro okhudza zimenezi).
 2. Kumuphunzitsa mwana mayina oyera a Mulungu ndi mbiri zake zomwe zimasonyeza kukwanira kwake kwa Mulungu ndi ubwino wake, ndipo Mulungu ndi wachifundo komanso wachisoni, yemwe chisoni chake chimakwanira chilichonse, ndipo Iye Mulungu ndi wokhululuka yemwe amakhululuka zolakwika, ndipo iye amakhululuka ndi kufufuta zolakwikazo, Iye ndi wopereka yemwe amapereka ngakhale popanda wina wake kupempha kapenanso chifukwa, ndipo iye ndi muongoli yemwe amaongolera akapolo ake ku zonse zothandiza, iye ndi wachikondi yemwe amakondedwa ndi kukonda , ndipo popanda chikaiko , kumudziwa Mulungu kumeneku kumamuthandiza iye kuti amukonde Mulunguyo (66).
 3. Tipewe kulankhula mau oti: mukapanda kumvera mau angawa Mulungu akulangani; Pali kusiyana komuphunzitsa mwana kuti Mulungu amamulanga yemwe akunyozera, ndi kulumikiza chilango cha Mulungu ndi kumvera Mulungu nthawi zonse, ndikumamuopseza nacho chimenecho, ndithu zimenezi zimamulepheretsa mwana kuganiza mwakuya ndi mwa ukadaulo wa Mulungu ndi ukulu wake, sizimafunikira pophunzitsa kudalira kumuopseza mwanayo za Mulungu, koma ndi zokakamizidwa kumuphunzitsa mwanayo kukonda Mulungu ndi kumukuza ndikumulemekeza (67), tisamupatse Mulungu zomwe zingabweretse chithuzi thuzi choipa cha Mulungu pa mwanayo.
 4. Mwana akamawaona makolo akupemphera mapemphero aswalaat ndi ena otero muzinthu zimene zili zokakamizidwa, kapena akuchinyalanyaza chinthu choipa (chaharam); kawiwri kawiri mwana amafunsa chifukwa chomwe akumapangira zimenezi, ndiye pakufunika kuti payankho lawolo papezeke zakutchulidwa za chikondi ndi kumvera Mulungu, ukhoza kukhala mphunzitsi poyendera kutsatira ndi kumukonda Mulungu wapamwamba mwamba, chifukwa mwana amatsatira makolo ake, izi ndi zimene zimadzala chikondi mmitima ya ana ndi kuwafotokonzera ana aja za Jannah ndi mitendere ya muyaya yomwe Mulungu wawakonzera akapolo ake olungama ku Jannah.
 5. Mwana akafika msinkhu womamvetsa matanthauzo a zinthuzomwe zili zokakamizidwa kwa iye; ndithu iye aphunzitsidwe kuti kumukonda Mulungu ndi kokakamizidwa; chifukwa Mulunguwolemekezeka ndiyemwe anatilenga ife mukalengedwe kolongosokandipo anatipatsa zosiyana siyana natiyika ife kukhala apamwamba kuposa zolengedwa zake zina, natipatsa mtendere wachisilamu(68),ndipo timuphunzitse mwana kuti mitendere yonse yomwe yatizungulira imachokera kwa Mulungu, timuphunzitsenso m’mene angatamandire Mulungu pamitendere imeneyi ndi kumuthokoza ndikumupemphanso zoonjezera, ndipo kuyang’ana mitendere yotereyi kumabweretsa chikondi(69).
 6. Kumuthandizira njira zomwe zingamuthandize kubweretsa chikondi cha Mulungu ndi mtumiki wake monga mau azichitochito ndi zina zotero (70)

Nsanamira ya chiwiri:

kukhulupirira angelo

Ndithu mu kukhulupilira mwa angelo mukupezeka zinthu izi:kuvomereza kuti angelowo alipodi, kukhulupilira omwe tawadziwa maina awo mwa iwo,kukhulupirira nkhani yoona iliyonse yokhudza iwo, komanso kuwakonda iwo. Ndipo ena mwa matanthauzo a maphunziro omwe akufunikira kuti adzalidwe mu mtima wa mwana okhudza angelo ndi monga:

 1. Kuwaphunzitsa kuti iwo (angelowo) ndi zolengedwa za Mulungu zinalengedwa kuchokera kudangalira, Aisha (Mulungu asangalare naye) anati: adanena mthenga wa Mulungu (saw) kuti: “Analengedwa Angelo kuchokera kukuwala (dangalira), ndipo zinalengedwa ziwanda kuchokera kumoto, komanso analengedwa Adamu kuchokera ku chomwe munauzidwa (kudothi).Apa zidzakhala zokwanira kungofotokoza mosonkhanitsa (general) ngakhale osafotokozera pakalengedwe kake.
 2. Kuwaphunzitsa maina a angelo omwe tikuwadziwa, ena mwa maina awo ndi monga: Jibril, yemwe ndi wodalilika komanso mtsogoleri wa angelo onse, ndipo iye ndi amene anavumbulutsa buku lolemekezeka la Quru’an(kuchokera kwa mulungu kunka kwa mtumiki Muhammad, pomwe Mikail ndi mngelo yemwe anapatsidwa ntchito yogwetsa mvula, ndipo Israfil yodzaimba lipenga tsiku la chiweruzo.
  Timuphunzitsenso mwana kuti kuli angelo omwe anyamula mpando wachifumu (arishi) wa Mulungu, kulinso ena omwe amalemba ntchito zathu, ndipo ena anapatsidwa ntchito yotitetezera kuzosiyana siyana padziko pano, ndi ena otero.
 3. Kumufotokozera kuti chiwerengero cha angelo ndi chochuluka zedi, ndikuti yemwe amadziwa kuchuluka kwawo ndi Mulungu yekha basi, ndipo iwo (angelowo) ndi zolengedwa zomwe zinapangidwa kuti zizingomvera Mulungu ndikupanga zokhazo zomwe Mulunguyo wazilamulira kuti zichite, ndi kuti aliyense mwa angelowo ali ndi ntchito yomwe anapatsidwa kuti azigwira ndipo sangaisiye ntchito imeneyo.
 4. Ndipo iwo sachimwa, iwo amapembedza Mulungu mosalekeza ndipo sapumira kapena kuipidwa ngakhalenso kudzikweza ndipo iwo amakonda anthu okhulupilira, kuwapulumutsa, kuwapemphelera kwa Mulungu, kuwatetezera; ndipo iwo amatsata malo omwe pakutchulidwapo Mulungu ndikumakhala nawo (anthu omwe akutchula Mulunguwo).
 5. Kuwapangitsa ana kuti azikonda angelo, izi zingatheke kudzera powapangitsa anawo kuti amvetse bwino za chibadwa cha angelo chokonda zabwino ndi chidwi chawo pa anthu okhulupilira, izi zidzadzala moyo wa ubale ndi chikondi mwa anawo pa zolengedwa za madalitso ndi zosachimwa zimenezi (angelo); chifukwa iwo amakhala akumuyeretsa Mulungu (Tasbeeh), kumupempha chikhululuko Mulungu (Istighfar), komanso kupempha zabwino kwa Mulungu (dua) kuti zipite kwa anthu okhulupilira ndiponso amawauza nkhani zabwino anthu okhulupilira omwe akhazikika pachoonadi namagwira ntchito zabwino kuti akalowa kuminda ya mtendere(Jannah), komanso angelowo amawapemphera madalitso anthu okhulupilira, kuwapulumutsa kuchokera kwa adani ndikuwalimbikitsa (71).
  Ndipo angelo ndi omwe amasunga ntchito za anthu, chifukwa Mulungu anawatumiza iwowo kudzatetezera akapolo ake, Mulungu akunena kuti “(Munthu aliyense) alinalo gulu (la angelo) patsogolo pake (omwe) amamulondera (ndi kulemba zomwe akuchita) mwalamulo la Mulungu”.
 6. Kuwaphunzitsa kuti kukhulupilira mwa angelo zimafunika kuwalemekeza, chifukwa iwo ndi akapolo a Mulunguolemekezeka, sanyozera lamulo la Mulungu ndipo chomwe Mulunguyo wawalamula iwo (angelowo) amapanga, ndipo ndizokakamizidwa kuwachotsera angelowo mbiri zimene siziri zoyenera pa iwo.
 7. Kulimbikitsa ukhondo wapathupi pa anawo, chifukwa angelo amanyatsidwa ndi zinthu zomwe anthunso amanyatsidwa nazo. Jabir mwana wa Abdullah (r.a) anasimba kuti mtumiki (saw) adati: “Munthu akadya anyezi kapena adiyo (mukulankhula kwina anati: munthu akadya anyezi, kapena adyo, kapenanso kurath (leek), asayandikire malo omwe akupempherera anthu (ochuluka), chifukwa angelo amayipidwa ndizomwe anthu amaipidwa nazo”.(muslim -564).
 8. Kuwafotokozera kuti kupezeka kwa angelo ndi kukhulupilira mwaiwo kuli ndizolinga zakuya zochuluka monga:
  • Kuti munthu adziwe kuti Mulungu ali ndi kudziwa ndi kuthekera kwakukulu komanso nzeru zapamwamba kwambiri.
  • Kuti msilamu adziwe kuti alindi chitetezo, podziwa kuti ali ndi asilikali omwe akumamutetezera ndi kumamupulumutsa kudzera muchilamulo cha Mulungu.
 9. Timudziwitsenso mwana kuti mgwirizano wathu ndi angelo pakalengedwe kawo, kupezeka kwawo, komanso mmene amatiyang’anirira, umamudziwitsa (mgwirizano umenewu) munthu kuti iye ndi wofunikira kwambiri komanso wamtengo wapatali, ndipo umachotsa mwaiye maganizo oti iye ndi wopanda pakekapena wonyozeka, ndi chimenechi munthu amadziwa mlingo wake, ndipo amayetsetsa kukwanilitsa udindo wake waukulu womwe anapatsidwa.

Nsanamira ya chitatu:

kukhulupirira ma buku a Mulungu

Ndithu mukukhulupilira mabuku a Mulungu mukuyenera kupezeka mfundo zikubwerazi:

 1. Kukhulupilira kuti pali mabuku omwe anatsika kuchokera kwa Mulungu, ndipo icho ndichimodzi mwa chifundo chachikulu cha Mulungu pa akapolo ake; chifukwa mugulu lililonse la anthu analitumizira buku loti anthu ake aongokere, ndipo malamulo ake amakhala olingana ndi anthuwo, choncho mwana afotokozeredwe momveka bwino kuti kutsitsa kwa mabuku kumeneku ndi mtendere waukulu zedi; chifukwa mabukuwo ndiwo amene atidziwitsa za Mulungu, zatsiku lomaliza, zabwino komanso zoipa.
 2. Kuvomereza maina amabuku omwe tikuwadziwa mwaiwo, monga: buku la (Suhuf) lomwe linavulutsidwa kwa Ibrahim, Torah kwa Musa, Zaboor kwa Davide (Daud), ndi Injeel (chipangano chatsopano) kwa Yesu (Issa) komanso Quru’an kwa Muhammad, madalitso ndi mtendere zipite kwaiwo onse.
 3. Kuti mabuku amenewa amavomerezana lina ndi linzake ndipo satsutsana kapena kusemphana, Mulungu akunena kuti “(buku la Qur’an) lomwe likuyikira umbonimabuku omwe adalipo patsogolo pake” (Surat Al Maida: 48).
 4. Kukhulupilira nkhani zomwe zili zoona m’menemo, ndipo kumudziwitsa kuti mabuku akale anasinthidwa ndi kusokonezedwa ndi anthu, chifukwa iwo (mabukuwo) anali ndi nyengo yoyikika komanso kwa anthu anyengo yokhayo basi, moti Mulungu sanawateteze mabuku amenewo ngati m’mene amaitetezera quru’an ayi.
 5. Kukhulupilira kuti Qur’an inabwera kudzafufuta mabuku akale onsewo, ndikuti malamulo a Quru’an ndiwo akuyenera kugwiritsidwa ntchito kufikira tsiku la malipiro, moti nzokakamizidwa kutsatira zomwe zalembedwa m’menemo, kuloleza zomwe zalolezedwa m’menemo, kugwiritsa ntchito mavesi achindunji ndi kuimika manja pamavesi ovuta kuwamvetsa, ndi kumalekeza momwe Quru’an yalekeza ndi chiphunzitso chake (72).

Zina mwa zinthu zofunikira kwambiri kuti zipezeke mukukhulupilira mabuku a Mulungu, ndi izi: kumpangitsa mwana kuti aloweze Quru’an yolemekeka kuyambira ali wang’ono, pambuyo pake- mwazomwe zimathandizira kuonjezera nzeru mwa mwana ndiko kuti- akwanitse kugwiritsa ntchito Quru’anyo, ndipo mphunzitsi adzadzitse mu mtima wa mwana nyengo ya mavesi a Quru’an, chifukwa Quru’an imatiyitanira kuti tizilingalira ndi kuganizira za kalengedwe ka thambo ndi nthaka, kalengedwe ka munthu ndi zomwe zatizungulira, ndicholinga choti chikhulupiliro chathuchikwere ndikuti maphunziro athu asakanikirane ndi ntchito, ndipo kuloweza Quru’an yathu yolemekezeka ndi kumva komanso kuwadziwa matanthauzo ake zimamufikitsa munthu pa nzeru zapamwamba zedi (73).

komanso zimazoloweretsa lilime la mwana kulankhula mwa mfundo zothyakuka ndi momveka bwino kwambiri, izi zimatheka pamene akukonza lilime lake powerenga quru’an mwadongosolo, komanso zimameretsa kuganiza mwa uzimu- monga: kuopa Mulungu ndikudzipereka mwathunthu kwa Mulungu, kufunitsitsa zabwino kuchokera kwa Mulungu, ndikufewetsa mitima ndi maganizo-, ndipo zimazoloweretsa mwana kugwiritsa ntchito maphunziro ndi miyambo ya mu Quru’an yolemekeka pa zichito chito zonse zamoyo wakewatsiku ndi tsiku, komanso zimaphunzitsa mwana kukhala ndi moyo woongoka ndi makhalidwe apamwamba, phindu linanso amapeza malipiro aakulu ndi ulemerero waukulu kuchokera kwa Mulungu wapamwamba mwamba pamene mwanayo akukhala nawo pa mabwalo oloweza Quru’an (74).

TINGAMULIMBIKITSE BWANJI MWANA KULOWEZA QUR’AN

 1. Timufotokozere maubwino a Quru’an ndi maubwino akuiloweza, a kuiwerenga ndi kuyiphunzira komanso ndi kuigwiritsa ntchito, monga m’mene ananenera mtumiki (saw) kunenakuti “Muziwerenga Quru’an chifukwa iyo idzabwera tsiku lachiweruzo kudzawapemphera (dua) omwe amaiwerenga”. ( Muslim- 804), anatinso mtumiki (saw): “adzauzidwa munthu wowerenga Quru’an kuti werenga numakwera kumwamba ndipo uziililira ngati m’mene umachitira uli padziko lapansi, ndithudi malo ako akakhala pamene utasiyirepo”. (Tirmiz-2914), anatinso (saw): “Fanizo la wokhulupilira yemwe amawerenga Quru’an ali ngati chipatso chonunkhira bwino komanso chokoma bwino, pomwe fanizo la wokhulupirira yemwe sawerenga Qur’anali ngati tende, sanunkhira koma amakoma bwino, pomwe fanizo la achiphamaso (munafiq) yemwe amawerenga Quru’an ali ngati chipatso chonunkhira kwambiri koma chowawasa kwambiri, ndipo fanizo la achiphamaso yemwe sawerenga Quru’an ali ngati chipatso chomwe chilibe fungo lililonse komanso chowawasa kwambiri” (Bukhar- 5427), ananenanso mtumiki (saw) kuti: “Wabwino kwambiri mwainu ndi amene waiphunzira Quru’an ndi kuwaphunzitsanso (Qur’an yo) anthu ena” (Bukhar- 5027), ndipo timutchulire zitsanzo zina za ophunzira ake (maswahaba) omwe amaikira mtima pa Quru’an, izi ndi njira zikulu zikulu zogwedezera mtima wofuna kutengapo mbali pa Quran (75).
 2. Tiwalembetsere m’masukulu ndi m’magulu olowezeramo Quru’an, mmizikiti, kapena kumufunira mphunzitsi wa Quru’an, kukonza zomulimbikitsira maphunziro akewo ndi mphoto, ndikukhazikitsa mipikisano kuti ana ophunzira azipikisana.
 3. Tikuyenera kuwafewetsera kalowezedwe kawo ka Quru’an kuchiyambi chawo ndicholinga choti aziikonda ntchito imeneyi,tiyambe ndi juzu amma chifukwa iyi ndi yomwe ili ndi masura aafupi bwino komanso omveka mofananirako katchulidwe, zomwe zimapangitsa kuti Quru’an ikhazikike mwa mwanayo mosavuta (76), ndipo masurah (ma chaputala) amu juzu amma amenewa amakamba kwambiri zachikhulupiliro, kotero amakonza chikhulupiliro ndi makhalidwe a anawo, komanso kuteteza moyo ndi thanzi lawo, chifukwa Quru’an yolemekeka ndi chikumbutso cholembedwa, kuonjezerapo pa izi, ndithu Quru’an imakonzanso lilime ndi kulionjezera kuthekera kofotokoza bwino polankhula.
 4. Kumayesetsa kufotokozera mwachidule Quru’an yo pamene mwana akuiwerenga ndi kuiloweza; ndicholinga choti ndime za mu Quru’an zitsegule mtima ndi nzeru zake, ndipo munthu aliyense asaganize kuti mwana si woyenera kumutanthauzira Quru’an ayi, chifukwa mwa mwana muli kuthekera kodabwitsa kwa kuloweza ndi kumvetsetsa (77).
 5. Timuphunzitsenso kuti Quru’an ndi machiritso, chifundo komanso madalitso, Mulungu akunena kuti “Ndipo tikumatumiza ndime zina za Quru’an zomwe ndi machiritso ndiponso ndi chifundo kwa anthu okhulupilira”. (Surat Al Isra: 82), ndi kuti yemwe angailoweze yonse kapena gawo lina la iyo; atha kudzichiza yekha ngakhalenso kuwachiza ena pogwiritsa ntchito Quru’anyo.

Nsanamira ya chinayi:

kukhulupirira atumiki

Ndithu kukhulupilira mwa atumiki ndiko kukhulupilira koti iwo sadanenepo bodza ndikuti zonse zomwe ankanena- kupatula pa zomwe anapekeredwa ndi anthu- ndi zoona komanso kukhulupilira maina a omwe tawadziwa mwaiwo, ndikuti Mulungu anawasankha iwo kuchokera mwa anthu awo, kuti akhale osiyana nawo pamakhalidwe ndi panzeru zawo, ndicholinga choti aziwauza anthuwo uthenga wa Mulungu, Mulungu akunena kuti “Ndipo sitidatumize mtumiki aliyense (ndi chiyankhulo china) koma ndi chiyankhulo cha anthu akewo kuti awafotokozere momveka bwino”. (Surat Ibrahim: 4), chifukwa mtumiki akanakhala wochokera mwa angelo anthu sakanamumvetsa, kotero sizoyenera kwa ife kusiyanitsa pakati pa atumikiwa pokhulupilira ena mwaiwo ndikuwakana ena, koma tiwakhulupilire onsewo, chifukwa atumiki onse amanena zoona pa utumiki wawo komanso amalamulira anthu awo zoona zokha zokha, ndipo iwo anali otetezedwa pa ntchito yawo yofalitsa uthenga wa Mulungu, koma sitikukakamizidwa kugwiritsa ntchito kupatula malamulo omwe anatsika kwa mtumiki womaliza wa iwo yemwe ndi Muhammad (saw), ndipo zina mwa mfundo zamaphunziro zokhudza chikhulupiliro chimenechi zomwe zikuyenera kudzalidwa mwa mwana ndi izi:

 1. Kuwalongosolera Ana kuti ndithu Mulungu anatumiza mu fuko (ummah) lililonse mneneri wochokera mwa iwo, kuti awaitanire anthuwo kuti azipembedza Mulungu mmodzi yekha ndi kuti azikanile zina zonse zomwe zimapephedzedwa zosakhala Mulungu, ndikuti atumiki onse ndi oyenera kuvomerezedwa, ochita ubwino ndi olungama, osamala malamulo a Mulungu ndi okhulupilika.

 2. Kufotokoza momveka kuti atumiki onse amaitanira ku zofanana zomwe ndi phata la kapembedzedwe ndi maziko ake,uku kunali kumupatula Mulungu kuti ndi wayekha pa mitundu yonse ya kupembedza- pa chikhulupiliro, mau ndi zichito chito-, komanso zochikanira chilichonse chomwe chimapembedzedwa chosakhala Mulungu.
 3. Kufotokozanso momveka bwino zolinga zomwe anatumizira aneneri kuzolengedwa zake, monga zolinga izi:
  • kuti zolengedwazo zimupembedze Mulungu yekha ndikumupatula kuti iye ndi mmodzi,
  • kuti awaongolere anthu kunjira yoongoka,
  • kwadziwitsa anthu zoyenera kuchita padziko pano za chipembedzo ndi za dziko lapansi komanso
  • kuwatulutsa mu mdima ndi kuwapititsa kudangalira,
  • kuwatsogolera anthu ndikukwanilitsa malamulo a Mulungu pa iwo,
  • ndi cholinga choti anthu azitsatira atumikiwo ndikumapanga zinthu zawo monga momwe atumikiwo akupangira.
 4. Pakuyenera kudziwa chifundo cha Mulungu wapamwamba mwamba ndi kuti iye amawalabadira akapolo ake; moti mpakana anawatumizira aneneri owaongolera anthuwo kunjira yake ndikuwalimbikitsa kuti azimuthokoza Mulungu wapamwamba mwamba pamtendere waukulu ngati umenewu, ndikuti aziwakonda atumiki ndi aneneri amenewa omwe anagwira ntchito yofalitsa uthenga wakewu ndi yolangiza akapolo ake, chifukwatu anthu angakhale atapatsidwa kumvetsa ndi nzeru zapamwamba bwanji sangakwanitse ndi nzeru zawo zokhazo kuika ndikuyendetsa ndondomeko yokomera anthu onse kukhala ogwirizana, othandizana ndi opereka china chilichonse kwa yemwe ali woyenera kupatsidwa, koma atumiki amaphunzitsa anthu zinthu za phindu kwa anthuwo komanso amawaletsa zomwe zingawapatse mavuto (78)
 5. Mudzalidwe kumukonda mtumiki (saw) m’mitima ya ana, kuti athe kumumvera ndikumutsata mapazi ake ndikumulemekeza, ndikutinso asakonde cholengedwa china chilichonse kuposa m’mene akumukondera mtumikiyo, komanso azikondana ndi okhawo amene amamukonda mtumiki, ndikudana ndi aliyense wodana ndi mtumikiyo (79),ndiponso azilemekeza dzina lamtumiki likatchulidwa namufunira madalitso ndi mtendere wa Mulungu, komanso azilemekeza mbiri ndi ma ubwino ake chifukwa iye anali wachifundo chochuluka komanso chisoni ndipo azimulemekezanso mtumikiyo akafika mwanayo kumanda ndi kumzikiti wamtumiki potsitsa mau ake- Mulungu akamudalitsa pompatsa zimenezi (kuthekera kokazonda manda ndi mzikiti wake {saw} ).

TINGAMUPHUNZITSE BWANJI MWANA KUTI AZIMUKONDA MTUMIKI(SAW)

 1. Tikuyenera kuwalongosolera motsindika kuti Mulungu wapamwamba mwamba amakonda mtumiki wake (saw), ndipo iye anamusankha ndikumulemekeza mtumikiyo kuposa anthu onse, ndipo Mulunguyo anatikakamiza kumukonda mtumiki ameneyo, ndipo timuphunzitse mwanayo kuti kumukonda mtumiki ndichizindikiro chomukonda Mulungu wapamwamba mwamba, moti yemwe angamukonde mtumiki ndiye kuti amamukondanso Mulungu mwachoonadi (80).

 2. Kumukumbutsa kuti mtumiki anali wachifundo kwa zolengedwa zonse powaongolera ndi kuwafikitsira chipembedzo chimenechi, ndipo azaonetsanso chifundo chimenechi pa okhuluplira powapangira pempho (dua ya shafa’a) tsiku lachimaliziro.
 3. Kumuwerengera nkhani zina zochokera mu mbiri ya mtumiki (saw) yonukhira ndi cholinga choti mwana adziwe kuti mtumiki ndi chitsanzo chabwino ndi chapamwamba choyenera kuti munthu wina aliyense azitsatira. Auzidwenso (anawo) zodabwitsa zomwe mtumiki anapanga, zikhalidwe zake zapamwamba, m’mene amawapulumutsira oponderezedwa, kufewa kwake ndi amphawi, ndi momwe amawalangizira anthu zochitira ubwino ana amasiye, komanso chifundo chake pa ofooka (81), ndipo izi zifotokozeredwe pogwiritsa ntchito mau ophweka molingana ndi msinkhu wamwanayo, ndipoosatuluka mu zomwe zikugwirizana ndi nzeru za anawo; ndicholinga choti azimvetse bwino ndi kuzisunga , ndipo tiyesetse kusintha njira ya kaphunzitsidwe ndicholinga chofuna kukwanilitsa zofunikira za msinkhu wa mwana molingana ndi misinkhu ya ana athu, komanso tionetsetse kusiyana komwe kulipo pakati pa ophunzira okha okha ndikusiyana kwanyengo yomwe ophunzirawo akukhala (82).
 4. Ana aziona pa makolo awo ndi anthu amene awazungulira kumulemekeza mtumiki ndi zichito chito zake komanso mau ake; potsatira mwachidwi zomwe mtumiki amachita, ndikumamufunira zabwino kwa Mulungu akamatchulidwa (mtumikiyo). Makhalidwe amakolo ndi zichitochito zawo, ndi imodzi mwanjira zikulu zikulu zophunzitsira mwana, nthawi ina iliyonse akapanga sunnah ina yake aziwauza ana akewo kuti: umu ndi mmene amapangira mtumiki (saw).

  Ndithu kuphunzira kudzera mukuonera kumapereka chithuzi thuzi pakaleledwe koona ka ana, komanso pachikhulupiliro cholongosoka, ndipo mtumiki (saw) ndicho chitsanzo chapamwamba chomwe aphunzitsi akuyenera kumachitsatira ndikuyenda muchiongoko chake komanso kukwanilitsa ma sunnah (ziphunzitso zake) moonekera limodzi ndi ana akewo (83).

 5. Kupangitsa mwana kuti aloweze ena mwa mahadith (mau amtumiki {saw}) oona omwe amasonyeza kuti chisilam ndi chokwanira komanso ndi chabwino, ndi omwe akusonyeza za makhalidwe a mbiri yabwino ya mtumiki ndi ophunzira ake( maswahaba ake),mahadith amapereka chizindikiro chachikulu pa chikhulupiliro ndi chikhalidwe komanso kukonza munthu (84), nzothekanso kuchititsa mipikisano bola mahadith ake akhale afupi afupi omveka bwino matanthauzo ake komanso okamba za makhalidwe ofunikira mu msinkhu wa ophunzirawo komanso ayetsetse kugwiritsa ntchito njira zachikoka, komanso mphatso ndikuyamikira munjira zosiyanasiyana.
 6. Kuwafotokozera ana nkhani za ophunzira ake (maswahaba) zonena momwe iwo amakhalira ndi kulemekezera mtumiki (saw) ndi nsanje yawo pa iye,makamaka pa Maswahaba omwe anali achichepere mwaiwo, monga nkhani ya Anasi (r.a) ndi kulimbikira kwake pomutsatira mtumiki (saw), monga tsiku limene telala wina anamuyitana mtumiki kuti akadye chakudya chomwe telalayu anakonza,Anasi adati:Ndinapita naye mtumiki (saw) kukadya nawo chakudya chimenecho ndipo anamubweretsera buledi wa tirigu, nsuzi, momwe munali nyama yang’ombe yophika komanso nyama yofutsa (yofwafwaza); Anasi adati ndiye ndinaona mtumiki akutsata nyama yofwafwazayo (dubaa-u) mumbale yonse, kuchokera tsiku limeneli ndinayamba kukonda (dubaa-u)”.
  Thumamah anasimbanso kuti Anasi anati: “Ndipo ndinayamba kumamusonkhanitsira mtumiki dubaa-u yo ndikumamuikira kumbali yake”. (Bukhar- 5439).
  kotero mphunzitsi ayesetse kulongosola mmene maswahabah (Mulungu akondwere nawo onsewo)amamukondera mtumikiyo ndi mmene amaziperekera nsembe panjira yake, ndipo awasimbire nkhani zosiyana siyana ngati zimenezi (85)
 7. Kumuphunzitsa zotsatira zakumukonda mtumiki wa Mulungu kumeneku, monga: hadith ya Anasi (r.a) yoti ndithu munthu wina anafunsa mtumiki (saw) za qiyamah kuti kodiibwera liti qiyamah (tsiku lachiweruzo) Mtumiki adati :Nchiyani chimene wapanga chokonzekera qiyamah?” munthu ujaanati: palibe chilichonse kupatula kumukonda Mulungu ndi mtumiki wake, apa mtumiki anati iwe udzakakhala ndi yemwe umamukonda” Anasi adati: sitidasangalatsidwepo ngati m’mene tinasangalalira ndi mau amtumiki akuti: iwe udzakhala ndiyemwe umamukonda , anatinso Anasi: ine ndimamukonda mtumiki (saw), Abubakar ndi Umaru, ndipo ndikulakalaka kuti ndikakhale nawo limodzi chifukwa chakuti ndimawakonda ngakhale sindimatha kugwira ntchitozangati zomwe iwo amagwira”. (bukhar- 3688).
 8. Kumuthandiza mwana kuti athe kuzitulukira mwaiye yekha zachilendo zokhudza kumukonda mtumiki, monga: kulemba ndakatulo, kankhani, ulaliki, nkhani (article) ndi kulimbikitsa mipikisano yosiyana siyana yokamba zakumukonda mtumiki (saw) (86).

Nsanamira ya chisanu:

kukhulupirira za tsiku lomaliza

Ndithu mukukhulupilira za tsiku lomaliza mukupezeka zinthu izi:
– kukhulupilira zainfa ndikuuka kwa akufa,
– kudzawerengedwa ntchito zathu ndi kudzalipdwa,
– ka mlatho kochepa kwambiri kakuthwa ngati (lezala) kamene azikaoloka anthu,
– sikelo (yomwe azikayezera ntchito za munthu),
– Jannah (nyumba ya mtendere) ndi moto.
Ndipo mwana amayamba kuzimvetsa bwino zina mwazithu zokhudza tsiku lomaliza akatha msikhu, ndipo ngati sanafike pa msinkhu umenewu ndi bwino kumawafotokozera mwachidule kwambiri, moti tizingomufotokozera kuti pa mbuyo pa moyo uno kuli moyo wina, ndikuti Mulungu analenga Jannah kukhala malo okakhalamo anthu okhulupilira, komanso moto kukhala malo okakhala anthu okanira (87).

Ndipo ena mwa matanthauzo amaphunziro omwe akuyenera kudzalidwa mwa mwana okhudza kukhulupilira za tsiku lomaliza ndi awa:

 1. Mwana adziwe kuti ndithu Mulungu wapamwamba mwamba, adzaukitsa akufa onse tsiku la chiweruzo kuti akapeze malipiro awo antchito zomwe anagwira padziko lapansi, ngati zinali zabwino akalipidwanso zabwino, koma ngati zinali zoipa akalipidwanso zoipa.
 2. Mwana adziwe kuti tsiku limeneli Mulungu wapamwamba mwamba adzapezeketsa Jannah yomwe adailenga kukhala malo a ulemelero, achisangalaro komanso amuyaya, kuti akhale malipiro a akapolo ake okhulupilira, ndiponso adzapezeketsa moto umene adaulenga kuwakonzera anthu okanira. Anawo aphunzitsidwe zimenezi powakopa za mitendere yomwe Mulungu anaika ku Jannah kuwakonzera anthu okhulupilira.
 3. Kumukambira mwana nkhani ya infa ndi tsiku lomaliza mofewetsa moonetsa chifundo cha Mulungu, chikhululuko chake ndi kufewa mtima kwake pa akapolo ake, ndi cholinga choti musachulutse maganizo oopsa mwa mwanayo (88). Izi zingatheke kuzilumikiza ndi zolengedwa zina zilizonse zamoyo zomwe zimadutsa ma sitejingati omwewa, koma kuti munthu ndi wopatulika, chifukwa Mulungu anamusankha iye pomupatsa malamulo ndi kumufewetsera zolengedwa zonse kukhala pansi pa ulamuliro wake, komanso anamulonjeza malipiro pazimenezi.
 4. Kumufotokozera mwana kuti ndithu Mulungu samalora kupondereza, ndipo samamusiya wopondereza osampatsa chilango ayi, komanso samasiyawoponderezedwa osam’bwezera zomwe waponderezedwazo ayi, sasiyanso wolungama osamupatsa malipiro abwino ayi, pomwe ife timaona anthu opondereza padziko lapansi pano mpaka amamwalira akuponderezabe, choncho pali moyo wina pambuyo pa moyo uno kumene adzalipidwe wolungama aliyense zabwino ndi kukalangidwa woipa, ndipo aliyense akapeza chomwe amayenera kupeza (89).

Nsanamira ya chisanu ndi chimodzi:

kukhulupirira za chikonzero cha Mulungu

Ndithu mukukhulupilira za chikonzero cha Mulungu mukupezeka zinthu izi:
– kukhulupilira kuti kuzindikira kwa Mulungu ndikokwanira,
– ndipo chopezeka chilichonse anachilemba kale chisanapezeke,
– zoti iye ndi Mlengi wa chilichonse,
– komanso kuti ali ndi chifuniro chokwanira.

Koma kuti mwana sangathe kumvetsa za chigamulo ndi chikonzero cha Mulungu pamene akadali wang’ono, ndipo ena amaonanso kuti mwana sangakwanitse kumva matanthauzo achigamulo ndi chikonzero cha Mulungu pokha pokha akapitilira zaka pafupi fupi zisanu ndi zinayi (9) zakubadwa kwake (90), koma pali mfundo zamaphunziro zomwe zikuyenera kudzalidwa mwa mwana zokhudza chigamulo ndi chikonzero cha Mulungu chimenechi, ndipo zina mwa izo ndi izi:

 1. Kuti ndithu phata la nkhani imeneyi ndi hadith yomwe inabwera kudzera mwa mwana wa Abbas yemwe ndi Abdullah bin Abbas, iye adati tsiku lina ndinali pambuyo pa mtumiki (saw) ndipo anati: “Oh mwana iwe, ndithu ine ndikufuna ndikuphunzitse mau awa: “Umusunge Mulungu ndipo iye akusunga, umusunge Mulungu umupeza patsogolo pako, ukafuna kupempha uzimupempha Mulngu, ukafuna thandizo uzipempha kwa Mulungu, ndipo dziwa kuti angakhale anthu onse atasonkhana kuti akuthandize pa china chake, sangakwanitse kutero pokha pokha pachokhacho chimene Mulungu anakulembera kale, ndipo atasonkhana kuti akuzunze ndi china chake, sangakwanitse kutero pokha pokha pachokhacho chimene Mulungu anakulembera kale kuti chikuzunze, zolembera zinanyamulidwa kale (zitalemba zimenezi), ndipo mapepala ake anauma”. (Tirmiz- 2516),Ndipo muhadith ina mtumiki (saw) anati: “Umusunge Mulungu umupeza patsogolo pako, udzipangitse kuti udziwike kwa Mulungu (pogwira ntchito zabwino) pamene uli pa mtendere, Mulungu adzakudziwa pamene uli pamavuto (adzakuthandiza), ndipo dziwa kuti chomwe chakuphonya si chinali choti chikupeze, ndipo chomwe chakupeza sichinali choti chikuphonye, choncho dziwanso kuti chipulumutso chimadza kamba kopilira ndipo kufewetseredwa kuchipsinjo kumadza pambuyo povutika kaye, ndipo pamene pali zopweteka pamakhalanso zokoma”, (Ahmad- 2803),, hadith ya mtumiki imeneyi imatengedwa kuti ndi gwero la maphunziro, ndipo muli ziongolero zabwino zochokera kwa mtumiki wolemekezeka (saw) kupita kwa anthu (ummah) ake onse za m’mene angamaonetsere chidwi pa kaleledwe kabwino ka ana awo pachukhulupiliro cholongosoka (91).
 2. Nzofunikira kwambiri kupewa kuilowa kwambiri limodzi ndi mwana nkhani ya chigamulo ndi chikonzero cha Mulungu pa msikhu umeneu, chifukwa zomwe mphunzitsi angathe kufikitsa kwa mwana pankhani imeneyi ndi monga izi:
  ∗ kufotokoza momveka bwino kukula ndikuya kwa kuzindikira kwa Mulungu kuyambira kale,
  ∗ kuti Mulungu ndi wakutha chilichonse ndipo wazungulira chilichonse,
  ∗ kuti iye ndi Mlengi wachilichonse,
  ∗ kuti iye ali ndikuthekera kwachina chilichonse chomwe wafuna.Ngakhalekuti munthuyonsoanamupatsa ufulu wosankha ndi udindowokwanira pa ntchito zake zodzisankhira, akuyenera kudzalipidwa zabwino kapena kulangidwa pazimenezi. Ndipomwana auzidwe izi mwachidule, koma ngati anawo atadzadzidwa ndi mafunso okhudza mutu umeneu, mphunzitsi azayenera kufotokoza m’mene angathere koma mwa mulingo wabwino womwe nzeru zamwanayo zingathe kuitolera nkhaniyi (kuimvetsa).
 3. Kumuphunzitsa mwana kuti azipempha kwa Mulungu osati kwa aliyense ayi, ndipo thandizo azipempha kwa Mulungu yekha, chifukwa Dua (pempho) iliyonse imayenera izilunjika kwa Mulunguwapamwamba mwamba kokha basi, aphunzitsidwe kuyedzamira mwa Mulungu yekha komanso kupilira pa chigamulo ndi chikonzero cha Mulungu.
 4. Mwana aphunzitsidwenso kuti Mulungu safunira iye (mwanayo) kupatula zabwino zokha zokha, moti iye (mwana) alipanyengo yomwe Mulungu anamuyikira iye kuti akhale padziko pano ndipo azikumana ndi zokhazo zomwe Mulungu anamukonzera, kotero moyo wake sungamakhale wobanika kapena wodandaula, ndipo azikhala wosangalatsidwa ndi chigamulo cha Mulungu akamakumana ndi zowawa (zokhoma), iye amakhulupilira ndi mtima wake wonse kuti: “Palibe chomwe chingatipeze kupatula chokhacho chimene Mulungu anatilembera” (Surat at Taubah: 51).
 5. Aphunzitsidwenso kuti Mulungu wapamwamba mwamba ndi yemwe amayendetsa chilichonse, ndipo iye amapangachomwe wafuna ndiponso amasankha chomwe wafuna, chifukwa iye ali ndi ufulu wopanga chilichonse mu ufumu wake ndi pazomwe amazilamulira. Izi zidzapangitsa kuonjezera mgwirizano wake ndi mbuye wake ndikulunjika kwa iye pazilizonse, zotsatira zake adzakoleka malingaliro, mapemphero (madua) ndi chiyembekezo chake pa Mulunguyo.
 6. Kukhulupilira za nsanamira imeneyi zimapangitsa mwana kukhala ndi mtima wosakondera ndi wodekha nthawi iliyonse yomwe wokhulupilira wadziwa kuti zonse zomwe zimamupeza (zabwino ndi zoipa) zonsezo zimakhala ndi ubwino paiye ndikuti palibe choipa champakana kale kale; zimenezi zimapangitsa mtima wa mwanayo kukhala wodekha ndi wokhazikika mkati mwake, izi zidzapangitsa iye kukumana ndi mavuto ake, zotopetsa zake ndi ziphinjo zake, ali ndi mtima wolandira chigamulo ndi chikonzero cha Mulungu, zotsatira zake amapereka zichito chito zake m’manja mwa Mulungu nakhala wodekha mu mtima ndim’maganizo momwe (92).
  Yemwe angakhulupilire chikhonzero cha Mulungu samadandaula kapena kusowa chochita, ndipo sapsa mtima pamavuto kapena zikamugwera zokhoma koma m’malo mwake amazipereka kwa Mulungu namayembekezera malipiro abwino kuchokera kwa Mulungu ndipo akamugwera mavutowo nthawi yomweyo amafulumira kutchula mau a Mulungu ngati m’mene akunenera mwini wake “Choncho auze nkhani yabwino opilira, omwe mavuto akawapeza amati ndithudi ife nga Mulungu , ndipo kwa iyeyo ndiko tidzabwerera, otero ndi amene ali ndi madalitso ndi chifundo chochokera kwa mbuye wawo, ndiponso iwo ndi amene ali oongoka”. (Surat Al Baqarah: 155- 157).
 7. Tingathe kuthandizana pobweretsa zina mwa nthano komanso tinkhani tomwe tikuonetsa kuti anthu ake anapanikizika ndi chikonzero cha Mulungu pa iwo, ndipo pambuyo pake anapeza zabwino chifukwa cha chikonzero chimenechi, moti mpakana zinthu ndi nyengo kwa iwo zinasitha napita ku ubwino.
 8. Chidule cha kukhulupilira muchikonzero cha Mulungu ndiko kukhulupilira kuti Mulungu amadziwa chilichonsemopanda kupatula (in general) ndi mwatsatane tsatane (in detail). Ndithu iye analemba zomwe anazidziwa nkale mwa zinthu zomwe zidzachitike mtsogolo monse pazolengedwa zake kufikira tsiku lachiweruzo, zimenezi adazilemba mu lauhul-mahfudh ndikuti zochitika zonse sizingachitike pokha pokha Mulungu akafuna komanso akachipanga.
Back to top button