MAFUNSO OKHUDZA MABUKU

Kodi mabuku akumwamba ndi ati?

Awa ndi mabuku omwe Mulungu adawavumbulutsa kwa atumiki ake (madalitso ndi mtendere a Mulungu zipite kwaiwo); ndi cholinga choti afalitse uthenga ndi kulamulira malamulo ali mmenemo, mabuku amenewa ndi chiongoko komansochifundo kwa zolengedwa zonse ndi cholinga choti zisangalale pa dziko lino lapansi ndi moyo womwe uli nkudza.
Ndipo zomwe tikudziwa zokhuda mabuku amenewa ndi zoti: Mulungu adabvumbulutsa kwa mneneri Ibrahim (Abraham) (a.s.) buku lotchedwa (Suhufu), kwa Daud (Davide) zaburi (masalimo), kwa Musa (Mose) Taurat {chipangano cha kale}), ndipo kwa Issa mwana wa mariam (Yesu) Injeel {chipangano chatsopano}), ndipo kwa Muhammad (Quru’an) (151).

KODI NCHIFUKWA CHIYANI TIMAFUNIKIRA QUR’AN? NANGA CHIFUKWA NINJI QUR’AN ILI CHOZIZWITSA CHA MUYAYA?

Ngati chipangizo chophweka chopangidwa ndi munthu chimafunikira ka buku kotidziwitsa mmene chipangizocho tingachigwiritsire nthito moyenera; ndiye kuti munthu – yemwe ndi chopangidwa (cholengedwa) ndi Mulungu- azafunikira kwambiri buku lomuongolera ndikumudziwitsa njira yachiongoko,kupambana ndi kulongosoka padziko la pansi ndi dziko lomwe lili nkudza, Mulungu akunena kuti: “Kodi asadziwe yemwe adalenga (zinthu zomwe adalenga)? Kumachita kuti iye ngodziwa zinthu zing’onozing’ono kwambiri ndiponso wodziwa nkhani zonse”. (surat Almulk: 14).

Komanso Quru’an ndi chodabwitsa; chifukwa mtumiki Muhammad (saw) ndi mneneri womaliza wa aneneri onse, choncho pakuyenera kuti chodabwitsa chake chikhale chopitilira mpaka kalekale, chifukwa palibeso mneneri wina pambuyo pake, ndiye pakuyenera kuti umboni ukhalepobe nthawi zonse, pakuyenera kuti tchalenji yake ikhalebe kufikira tsiku lachiweruzo.
Ndipo maumboni osonyeza kuzizwitsa kwa Qur’an ndi ochuluka zedi, ofunikira kwambiri mwaiwo ndi awa:
kuzizwitsa kwake pachilankhulo ndi kulongosoledwa bwino kwa mfundo zake, ndipo ichi ndichimene Mulungu anawatchalenja nacho aluya omwe anali otsogola pakulongosola ndikumveka bwino mau polankhula, koma anthu ndi ziwan-da zonse zinalephera kupeka mau angati a mu Qur’an imeneyi yolemekezekayi. Uwu ndi umboni woti Quru’an imeneyi inachokera kwa Mulugu (152).

Kodi chifukwa chiyani Mulungu sanawatetezenso mabuku akalewa?

Ndithu Mulungu wapamwamba mwamba amapanga zomwe akufuna, ndipo amakhala ndizolinga za nzeru zakuya, zina mwa izo timazidziwa ndipo zina sitimazidziwa, koma maumboni omveka akuonetsa poyera kuti mabuku akalewo sadali chozizwitsa, choncho sichidali chofunika kuti apitilire, komanso iwo anali malamulo anthawi yochepa ndi kwa anthu ochepa (153).

Kodi ndi maumboni ati omwe akutsimikizira kuti Qur’an siidasinthidwe kalikonse?

Funso ngati ili nthawi zambiri omwe amakonda kufunsa ndiomwe ali a msinkhu woyambira pakatikati ndikumapita mtsogolo, kotero tidzayenera kumulongosolera modekha ndi momuunikira mwanzeru zomwe zingatsindike kuti Qur’an ndi yoona, kenako timuuze kuti: ndithu zinthu zikanenedwa mobwerezabwereza ndikuchitika kambirimbiri zimakhazikika ndipo zikafala zimatsimikizika, ndipo Qur’an inatipeza kudzera munjira yofala (yowanda), ndipo timulongosolere tanthaunzo lakufalako ( التواتر ) kuti ndikulandilidwa nkhani ndi gulu lochuluka kuchokeranso ku gulu lochuluka losatheka kumveka ndi bodza, adziwe zimenezo anthu wamba ngakhalenso anthu odzitsata, ndipo asilamu anatengera zolandila nkhani zimenezi m’bado kuchokera ku m’bado wina, amaphunzitsana Qur’an imeneyi mokhala mwawo, amaiwerenga m’mapemphero awo, ndipo amawaphunzitsanso ana awo, moti titati tiyerekeze kuti munthu wophunzira wamkulu ndi wolemekezeka kwambiri komanso woopsa atati alakwitse chilembo chamu Quru’an mo, ana adzamudzudzula iye akulu akulu asanamudzudzule, choncho kufikira inatipeza ife Quran imeneyi ilibe choonjezera kapena chopunguka, ili yotetezeka yosasindidwa.

Atati atsuste mwanayo umboni umenewu ndiye kuti adzathanso kutsutsa maumboni ena onse omwe ali okhazikika ndi oona, monga kupezeka kwa mtumiki, ophunzira amtumiki (maswahaba) ndi anthu ena odziwika mumbiri yachisilamu, zoterezi ngakhale anthu anzeru onse sangagwirizane nazo (zotsutsa umboni umenewuzi), ndipo mu Qur’an Mulungu adawatchalenja anthu ndi ziwanda kuti abweretse chofanana ndi Qur’an yo ndipo sanakwanitse, ndipo mu Qur’an yonse mulibemo kusemphana kapena kukhulana ngakhalenso kupelewera ndipo kudabwitsika kwa nkhani zake, malamulo ndi mau ake ……. Zikusonyeza kuti ndithudi Qur’an yo sidachokere kwa munthu, chifukwa munthu ntchito zake komanso mau ake amasintha sintha komanso kupunguka; Qur’an yo inachokera kwa Mulungu ndipo iye anatenga yekha udindo woyiteteza (154).

Back to top button