MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPILIRA TSIKU LOMALIZA

Kodi tsiku lomaliza ndi liti?

Ilo ndi tsiku lomwe Mulungu adzaukitse zolengedwa zonse kuti akaziwerengere ntchito zake, ndipo limatchedwa lomaliza chifukwa palibenso tsiku lina pambuyo pake, ndipo limatchedwanso kuti ndi tsiku lamalipiro chifukwa Mulungu akawalipira anthu patsiku limeneli pa zintchito zomwe adatsogoza ali padziko lapansi lino, kotero yemwe angagwire ntchito yabwino kapena yomvera Mulungu ndiye kuti Mulungu akamulowetsa iye ku Jannah, ndipo yemwe angagwire ntchito zoipa nanyozera malamulo a Mulungu; Mulungu akamulowetsa iye ku moto, ndipo ili ndi tsiku lomwe lidzakhale lomaliza paumoyo wa padziko lapansi ndi kwa anthu onse. Tsikuli limatchedwanso kuti louka, kutanthauza kuti: patsiku limeneli anthu adzauka m’manda kulunjika kumwamba kuti akawerengeredwe ntchito zawo[1].

Kodi tsiku loukali lidzabwera liti? Nanga nchifukwa chiyani Mulungu anatibisira tsiku limeneri?

Palibe amene akudziwa kuti tsikuli lidzabwera liti, Mulungu akunena kuti: “Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuopa; (osati kulengeza za nthawi)” (Surat Annazi’ati: 45), Mulungu anatibisira tsiku limeneli ndi cholinga choti tilimbikire kugwira ntchito ndikukhala okonzekera tsiku lililonse, pogwira ntchito zabwino ndi kusiya ntchito zoipa; ndipo munthu akanadziwa tsiku limeneri lobwelera kwambuye wake sakanalapa kufikira nthawi itasala yochepa, ndipo dziko likanadzadza ndi zoipa kuposa m’mene liliri panopa[2].

Kodi kuwerengetseredwa ndiko kutani?

Uku ndi kusonkhanitsa komwe Mulungu adzasonkhanitse anthu onse oyambilira mpakana omalizira, Mulungu akunena kuti: “Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo) kuti ndithu, amibadwo yoyamba ndi yomaliza omwe inu muli m’gulu lawo adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa” (Surat Al Waqi’ah: 49-50), nawaonetsa ntchito zawo ndikuwalipira molingana ndi momwe anagwilira ntchitozo, munthu yemwe angagwire ntchito yabwino akalipidwanso zabwino, ndipo yemwe angagwire ntchito yoipa adzalipidwanso zoipa, Mulungu akunena kuti: “ Choncho amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono azaona malipiro ake, ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, azaona malipiro ake” (Surat Azilizaal: 7-8).

Kodi infa ndi chiyani?

Ndithu mwana wazaka zisanu ndi chimodzi ndikumatsika – nthawi zambiri- sangathe kumvetsa tanthauzo leni leni lainfa ndi kuuka kwa akufa.Komano zoona zake ndizoti infa ndi mathero eni eni amunthu wina aliyense pa umoyo uno, pomwe mwana wazaka zisanu ndi chimodzi kufikira wazaka zisanu ndi zitatu angathe kumvetsa nthawi zambiri- tanthauzo lainfa komanso zoti idzakhudza anthu onse, ndipo mwana woyambira zaka zisanu ndi zitatu kufikira zaka khumi; angathe kumvetsa mokwanira nkhani ya ifa ndikuuka kwa akufa, amatha kuona kapena kumva nthawi zina amatha kudutsana ndi nyengo ya infa m’banja mwake, nakhala kuti kumemeko ndikukumana kwake koyamba ndi infa, koma sitikudziwa m’mene angadzamvere kapena adzakhuzidwire akadzamva za infa ndi manda, zachidziwikire adzadzadzidwa ndi mantha chifukwa chakutchulidwa zinthu zimemezi; choncho tikuyenra kumulongosolera mwana za infa mosamunamiza komanso mogwira mtima mpaka akhutitsidwe kuti munthu womwalira amakhala kuti, ali paulendo- mwachitsanzo- munjira imeneyi mwana adzadziwa zenizeni kuchokera kwa anthu ena mwachangu. Ndipo ndi bwino- mwana asanakumane ndi banja lomwe lili munyengo ya infa timudziwitse kapena timuonetse mbalame yakufa kapena mtengo wakufa, chifukwa zimenezi zidzamuwalitsira tanthaunzo la ifa mwa njira yokhudzika, kenako tiyetsetse kumulongosolera mwanayo mwachidule kuti ndithu munthu akamwalira amapita kukakhala mu umoyo wina, ndipo tonse tidzamwalira ndipo tidzakakumana ndi onse omwe adamwalira ndi kukhala nawo ku mtendere Mulungu akadzalora. Ndipo ndizofunika kuti mwana adziwe kuti ndithu infa simathero amunthu ayi, koma kuti ndi kusuntha kuchoka kwa munthu wokhulupilira kunka ku umoyo wabwino ndiwapamwamba kwambiri, komanso kusuntha kwa munthu woipa kukakumana ndi malipiliro azoipa, ndipo Mulungu akamatenga moyo wathu (kutipha) sizimatanthauza kuti Mulungu samatikonda ayi, koma amatenga moyo umeneu ndicholinga choti tikakhale naye pafupi m’minda yapamwamba komanso yokongola kwambiri yomwe kukongola kwake sitingathe kukuyerekeza[3].

Kodi chifukwa ninji ana ena amamwaliranso?

Ana nthawi zambiri sapanga zoipa, ndipo salakwitsa mwadala, pachifukwa chimenechi; Mulungu amawalandira iwo mwachifundo nawalowetsa ku Jannah,ndipo munthu akamwalira naola,ndithu mzimu wake umakhalabe moyo chifukwa umakwera kupita kwa mlengi wake, ndipo mbiri ndi ntchito zake zabwino zimatsalirabe mmitima ya anthu, choncho, ndithu munthu akuyenera kukonzekera kukakumana ndi mbuye wake popanga zabwino ndi kugwiritsa ntchito maphunziro ndi malamulo a chisilamu[4].

Kodi tikamwalira timapita kuti?

Nthawi yathu yomwe Mulungu anatiikira kuti tikhale pa dziko pano ikatha; timasuntha kupita kumanda- awa ndi malo okhala akufa okhaokha-, ndipo mandawa atha kukhala bwalo mmabwalo aku Jannah kwa munthu yemwe angakhulupirire  mwa mbuye wake, kumumvera malamulo ake , ndikugwira ntchito zabwino pamene ali moyo pa dziko la pansi, adzasangalala mmandamo kufikira tsiku louka kwa akufa[5].

Kodi wakufa amamva kapena amaona?Nanga amapuma bwanji munthaka? Nanga amadya kapena kumwa ndi kugona?

Inde wakufa amamva salaam tikamawapatsa, amawafikanso mapemphero anthu tikawapemphelera, koma sapuma ngati ife ayi chifukwa iwo samafunikira kupuma, chifukwa iwo ali moyo wina wosiyana ndi moyo wathu wadziko lapansiwu, choncho; moyo umene uli nkudza umayambira m’manda, umakhala ndi dongosolo lake lake ndi chibadwa chake chake chosiyana ndi moyo uno, kulibe kupuma, kudya, kumwa, kugona ngakhale kugwira ntchito zina, koma kusangalala kwa mpaka kale kale, kapena zilango zampaka kale kale[6].

Kodi Jannah nchiyani? Nanga mu Jannah mo muli chiyani?

Jannah ndi nyumba ya mtendere, ndi malo okongola komanso kuli chilichonse chimene umachilaka laka ndi chomwe umachikonda. Jannah ndi malo omwe amapita anthu olungama omwe amamgwira ntchito yabwino, Jannah ili ndi makomo asanu ndi atatu (8) komanso osanjikizana opita m’mwamba, azikalowa anthu okhulupilira molingana ndi mulingo wa ntchito zake zabwino ndi chifundo cha Mulungu pa iye, yemwe adzakhale ndi ntchito zabwino zochulukitsitsa adzakhalanso pamalo okongoletsetsa ndi apamwamba kwambiri kuposa wa ntchito zochepa, komabe onse adzakhala osangalala, okondwera komanso moyo wa mtendere, mu Jannah tizikahalamo osangalala, sitidzadwala ngakhale kutopa, tikamuonako Mulungu, mtumiki (saw) ndi aneneri onse kuphatikizapo ndi onse amene timawakonda- Mulungu akadzalola-, kumeneko kuli chilichonse chimene tingachikonde ndi kuchifuna, kuchokera muchakudya ndi chakumwa, chisangalalo ndimitendere[7].

Kodi moto ndi chiyani? Nanga nchifukwa chiyani Mulungu adaulenga moto umenewu?

Moto ndi nyumba kapena malo azilango, ndipo ndi malo omwe Mulungu anawakonza ndi cholinga choti akawalangiremo onse ogwira ntchito zoipa kapena kuzunziramo anthu onyozera Mulungu, omwe samamvera malamulo ake.

Kodi zinyama zikalowa kuti? Ku Jannah kapena ku moto?

Zinyama sizinalamulidwe malamulo, koma izo ndi zolengedwa zomwe Mulungu adazipeputsa kuti zitumikire anthu, moti izo sizidzawerengedwa kapena kulangidwa ayi, tsiku lachiweruzo Mulungu adzazisonkhanitsa zinyama zonse naziuza kuti zibwezerane zina ndi zinzake zomwe zidalakwirana padziko lapansi, moti mbuzi yopanda nyanga adzaiuza kuti ibwezere ku yanyanga yomwe inaibaya iyo, Mulungu akadzamaliza kuzilamulira zinyamazo kubwezeranako adzazilamula kuti zisanduke dothi! ndipo zidzatero[8].

2  Al as-ilatu al aqaidiyah in-dal atwifal wal ijabat alaiha, Dr. Bassam al ‘amoosh, tsamba: 68.

2 Al as-ilatu al aqaidiyyah in-dal atwifal wal ijabat alaiha, Dr. Bassam al ‘amoosh, tsamba: 67.

1  Twifluka wa as-ilatuhu al harijah, Shaahiinaaz Abdul Fattah, tsamba: 76.

2  Asiilatu twifulika al harajah, Abu majid harak, page 170.

3   Min al yaum lan tahruba min as-ilati twiflika al muhrijah, Abdullah al mu’utwii, tsamba:159.

2    Al as ilatu al aqaidiyyah in-da al-atwifal wal ijabat alaiha, Dr. Bassam al ‘amoosh, tsamba:79.

1  As-ilatu twiflika al harijah, Abu majd harak, tsamba: 27.

2   Al as-ilatu al aqaidiyyah in-dal atwifal wal ijabat alaiha, Dr. Bassam al ‘amoosh, tsamba: 81.

Back to top button