MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPIRIRA MWA ALLAH

MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPIRIRA MWA ALLAH

Ndithu mafunso omwe amakonda kuzungulira kwambiri mmutu wa mwana akakhala wachichepere kwambiri ndiwo mafunsa okhudza Allah. Ndipo pano tibweretsa ambiri mwa mafunso amenewa omwe ana amakonda kufunsa kwa makolo awo:

Funso Kodi Allah (MULUNGU) ndi ndani?

Choyamba, tisadikire kuti mpakana mwana atifunse zokhudza Allah,koma timufotokozere mwachangu za Allah nthawi zonse komanso pa zochitika ndi pampata (opportunity), ndithu yankho lolondola la funso la mwana lokhudza Allah ndi mbiri zake lidzamanga maziko a Tauheed( umodzi wa Allah) ndi kukhulupirira Allah ( mwini ulemelero wonse) mu nzeru za mwana komanso mu mtima wake,pachifukwa chimenechi, ndithu njira ya pamwamba kwambiri ndiko kuzipanga nzeru za mwana kuti zisiye kuganiza za maonekedwe a Allah mwini wakeyo koma aziganiza za mitendere ndi kudabwitsika kwa chilengedwe zomwe Allah walenga zomwe zikusonyeza kuti Allah alipo, monga kumwamba ndi thambo,nyenyezi, dzuwa ,mwezi,nyanja ,mitengo, ndi zina zotero (128),

ndikumudziwitsa ma ubwino a Allah pomulenga iye ndikumulengeranso ziwalo, monga :maso, makutu,pakamwa , lilime,mikono, miyendo ndi ziwalo zake zina. Ndipo timuuze kuti mitambo imeneyi anailenga ndi Allah, chimodzimodzinso nthaka, mitengo yonse, ndi zina zotero, kufikira mwana atazolowera ndikusangalatsidwa nawo mawu amenewa, ndipo akamatifunsa kuti kodi Allah ndi ndani? Tizimuyankha mwa chidule kuti iye (Allah) ndi amene adalenga anthu ndi zinthu zonse zomwe zatizungulira, kenako timupatse zitsanzo zochuluka pa chimenechi.

Tikamaliza kumudziwitsa ndi kumuonetsa zolengedwa za kumwamba ndi za pansi pano, namudziwitsa dongosolo ndi kasanjidwe ka ukatswiri ka zinthu zimenezi, tidzamuuze mwanayo kuti: kodi waliwona dongosolo la kasanjidwe kameneka, ndithu yemwe anapanga zimenezi ndi Allah, ndithu tikatero iye adzamudziwa mbuye wake mozindikira ndi mwa maumboni. Timuuzenso kuti Allah ndi amene analenga chilichonse ndipo iye (Allah ) safanana ndi chilichonse, ndipo iye ndi wachifundo, wodyetsa ndi wopereka, komanso ali ndi maina ndi mbiri zabwino ndi za pamwamba zokha zokha, choncho iye akuyenera kupembedzedwa ndipo asaphatikizidwe ndi china chilichonse, komanso timuuze kuti Allah amakonda kwambiri ana moti anawalamula akuluakulu kuti azithandiza , kuyanganira ndikuchitira ubwino ana ndi anthu onse,ndipo iye akatiwerengera pa ntchito zomwe tagwira zabwino ndi zoipa zomwe potilipira sawab (zabwino) kapena chilango, moti iye ndi amene amamulipira munthu wochita zabwino molingana ndi ubwino wake, komanso woipitsa molingana ndi kuipitsa kwake. Ndipo ndi bwino kuwaphunzitsa anawo ma Surah (ndime za mu Korani zazifupizifupi; chifukwa masurah amenewa ali ndi mayankho abwino abwino okhudza Allah ndi mbiri zake, moti iye ndi Allah yemwe: sanabereke kapena kuberekedwa, ndipo alibe wofanana naye (129).

Nzothekanso kumufunsa funso loti: “kodi ndi ndani yemwe anakugulira zovala zokongola zimenezi?”Ndipo iye adzayankha kuti: “bambo anga”, nanga ndi ndani yemwe amakuperekeza popita ku sukulu? Iye adzayankha kuti bambo anga, nanga ukadwala ndani amene amakuperekeza kwa dotolo? Iye adzati bambo anga, nanga ndi ndani yemwe amakutenga kupita kokasangalala nthawi ya tchuthi? Iye adzati bambo anga, nde kuti bambo ako ndi amene amakupangira zonse? Iye adzati: inde.

Zikatero muuzeni mwanayo kuti tsono Allah ndi amene amatiyang’anira tonsefe (iweyo, ife kuphatikizanso bambo akowo), iye ndi amene analenga chilichonse, zonse zomwe umaziona mmbali mwako ndi zolengedwa ndi Allah, dzuwa ndi mwezi, mitambo, Nyanja ndi mapiri, kulenga anthu,zinyama ndi mbalame, kulenga angelo ndi ziwanda,Allah ndi amene analenga dziko lonseli, ndipo Allah ndi wopereka komanso wachifundo, amatiyanganira ndi kutisamalira, amatikonda ndi kumatibweretsera maubwino nthawi zonse.

Funso Kodi Allah amafanana ndi munthu Him?

Ayi safanana naye,iye safanana ndi chilichonse, iye ndi amene analenga ine, iweyo ndi anthu onse, analenga mitengo, mitsinje,Nyanja ndichina chilichonse pa dziko lapansi pano, kwa iye ndi kumene kumachokera mphamvu za pamwamba , akafuna china chake amangochiuza kuti: ”chitika” ndipo chimachitikadi. ndipo Allah ndiwosiyaniratu ndi munthu, munthu sangathe kulenga munthu nzake, koma Allah zimenezo amakwanitsa, ndipo angathe kupanga chilichonse chomwe wafuna, nde chifukwa cha kuti palibe amene angathe kumuona Allah pa umoyo uno wa dziko la pansi, palibe amene angamufotokoze Allah (maonekedwe ake), ife sitingakwanitse kumuona Allah (chifukwa iye) ndi dangalira lamphamvu, kuthekera kwa maso athu ndi koperewera.

kenako timpemphe mwanayo kuti apite akayang’ane ku ma dangalira (rays) adzuwa ndipo asakasinzine ayi, kenako timufunse kuti: kodi ungakwanitse kuyang’ana (china chake) ku dzuwako? Ndipo iye adzatsutsa, choncho tidzamuuza kuti: mwana wanga wolemekezeka, dziwa kuti dangalira lochokera kwa Allah sitingathe kukwanitsa kupilira kuliyang’ana, koma tikakalowa ku Jannah tikamuona Allah muchilolezo chake.

Pamenepa mwana atha kukutsutsa ndi kuonetsa kusakhutitsidwa ponena kuti: zimatheka bwanji Allah yo osafanana ndi chilichonse? Apa pazafunika kumuuza mogwira mtima koma modekha ponena kuti: ndithu nzeru zathu ngakhale zitakhala zazikulu ndi zomvetsetsa kwambiri chotani,zidzakhalabe nzeru za umunthu ndizosakwanira, zimadziwa zokhazo zomwe Allah anafuna kuti zidziwe, ndipo zomwe Allah sanafune kuti nzeru zathu zidziwe sizingadziwe, moti nzosatheka kuti tidziwe zinthu zonse, chifukwa tidzakhalabe anthu. Timuuzenso kuti: Allah akanakhala munthu ngati ife nde kuti bwenzi akumadwala monga mmene ife timachitira, bwezinso akumadya, kumwa ndi kumwalira ngati mmene anthu amachitira, koma Allah samapanga nawo kapena kumuchitikira chilichonse mwa zimenezi, iye ndi wopezeka nthawi zonse, ndipo iye ndi mlengi wa mitambo, nthaka ndi chilichonse chimene chili pa dziko pano, choncho Allah safanana ndi chilichonse.

Tingathenso kumufunsa mwanayo kuti: kodi ifeyo anthu tingathe kuchiuza chinthu kuti “chitika!” nachitikadi? Mwana adzayankha kuti ayi, zikatero ife limodzi ndi mwanayo tidzatulutsa ganizo loti: ndithudi Allah simunthu ngati ife ayi koma iye ndi mlengi wamkulu kwambiri. Timuuzenso kuti kumva kwathu kuli ndi malire, timangomva zokhazo zimene zikupezeka pa mtunda wina wake, tikanakhala kuti timamva china chilichonse tikanatopa, maso athunso ndi ofooka, timangoona zokhazo zimene zili pa mtunda wina wake, ife sitingathe kuona zomwe zili kuseli kwa chipupa – mwachitsanzo-, ndiye mmene kulili kumva ndi kuona kwathu kuti ndi kofooka, chimodzimodzinso nzeru zathu ndi zofooka chifukwa sizimazindikira zinthu zonse (zimangozindikira zinthu zochepa zokha).

Ndithu nzeru za munthu ndi zofooka, moti kuyambira pamene Allah adalenga munthu kufikira lero, gawo la zimene munthu samazidziwa limakhala lalikulu kwambiri kuposa gawo la zomwe amazidziwa, ngakhale nzimu womwe umapezeka mthupi la munthu ameneyu –mwachitsanzo – ngakhale tili nawo pafupi kwambiri, koma sitimaudziwa kwenikweni kapena kuuyerekeza ndi china chake,ngati izi zikuchitikira pa chomwe chili mwa ife, kuli bwanji za chomwe chili kunja kwa ife?, kotero, ndithu nzeru za munthu zidzakhala zofooka , sizingathe kudziwa mmene Allah amaonekera; kotero maonekedwe a Allah sungawadziwe kudzera mu zithunzi kapena , nzeru ndi kuganizira chabe ayi, koma kudzera mu malamulo a Allah okha tingathe kudziwa,Quru’an yanenetsa zimenezi motere: “ Palibe chilichonse chofanan ndi iye, iye ndi wakumva zonse komanso amaona zonse”. (Surat Ash Shura: 11).

Kuchokera pa mawu amenewa, tikupeza kuti ndithu Allah safanana ndi ifekapena chilichonse (130), zimenezi zikusonyeza kuti Allah ndi wamkulu kwambiri yemwe tikuyenera kumukonda, kumupempha komanso kumuopa, ndipo ukulu umenewu ukukwanira kupangitsa kuti kukamuona iye ku Jannah kukakhale chonyaditsa chapamwamba kwambiri mu Jannah yonse.

Funso Kodi yemwe adamUlenga Allah ndi ndani?

Zikadakhala kuti alipo yemwe adalenga Allah,inenso nkadafunsa kuti: ndani adalenga mlengi? Sichoncho? Kotero tikuyenera kudziwa kuti zina mwa mbiri za mlengi ndi zakuti: iye sadachite kulengedwa ndipo iye ndi amene adalenga zolengedwa zonse, akadakhala kuti iye adachita kulengedwa sitikadamupembedza kapena kutsatira chiphunzitsondi malamulo ake, ndiye funso lonena kuti ndani adamulenga Allah silolondola ndipo lilibe tanthauza, mwachitsanzo, mmodzi wa iwo atakufunsa kutalika kwa nzere wachinayi wa chinthu cha mizere itatu (triangle)? palibe choyankha pamenepo chifukwa triangle ili ndi mizere itatu yokha, nde pamene pakulakwika mu funso loti analenga Allah ndi ndani? Ndi liwu loti: “adamulenga” lo motsogozedwa ndi liwu loti: “Allah”lo, chifukwa mawu amenewo sangayendere limodzi ayi, chifukwa wopembedzedwa salengedwa, ndipo ntchito yolengedwa ndithudi imakhala pa zolengedwa pokha, palibe amene angakwanitse kumulenga Allah, akadapezeka ameneyo nde kuti Allah nayenso akadakhala cholengedwa, koma Mulugu ndi wopezeka nthawi zonse, alibe chiyambi ngakhalenso mathero.

Olo titayesera kuika mtsutso woti kuli mlengi wa Allah(wapamwambamwamba), ndiye kuti anthu azingofunsana funso lomweli loti adalenga mlengi ndani? Choncho lizingopitilira osafika pa mathero a mtsutsowo, zosatheka kupezeka mlengi wa mlengi, ndipo pofuna kuyandikitsa zedi titenga chitsanzo cha msilikali ndi chipolopolo, iye akafuna kuombera azipemha chilolezo kwa nzake yemwe ali kumbuyo kwake, nayenso kuti apereke chilolezo akuyenera kupempha chilolezocho kuchokera kwa amene ali kumbuyo kwake, ndikumayenda choncho mpaka kopanda polekezera, funso nkumati: kodi msilikali uja adzaombera? Yankho nkumati: ayi, chifukwa sadzapeza msilikali yemwe adzapereke chilolezo choti iye awombere, pomwe tcheni chija ngati chingafike pa munthu yemwe pamwamba pake palibenso wina woti angapereke chilolezo chowombera ndiye kuti adzaombera, koma kupanda kupezeka munthu ameneyu, ndiye kuti anthuwo olo atachuluka motani chipolopolo chimenecho sichidzaombedwa, iwo adzakhala ngati ma ziro (zero) ukawandanditsa, olo atachuluka mopanda mapeto, iwo adzakhalabe opanda nambala ya chilendo(adzakhalabe ziro), pokha pokha kutaikidwa kumayambiriro kwakeko nambala ina yosiyana ndi ziro, monga (1) ndi manambala ena (131).

Funso KODI ALLAH ADACHOKERA KUTI NANGA ALI NDI ZAKA ZINGATI?Kodi Allah asanapezeke kunali ndani?

Ngati iwe – m’bale wanga wolemekezeka – ukudziwa kuti Allah sadalengedwe; ndithudi chimodzimodzi iye sadabeleke kapena kubelekedwa, alibenso chiyambi ngakhalenso mathero, kotero alibe zaka zakubadwa ngati momwe zikhalira kwa ife anthu, chifukwa Allah ndiye mlengi wamkulu wolemera kwambiri, mwini mphamvu komanso wolimba, mwini ulemerero ndi wachifundo yemwe ali ndi maina abwino okhaokha ndi mbiri zabwino komanso zokwanira osati zopunguka, Allah ndi amene anapezeketsa dzikoli ndi zolengedwa zonse.

Funso limeneli ndi chimodzimodzi ndi lija lonena kuti adamulenga Allah ndi ndani, ili ndi funso lolakwika chifukwa Allah ndi woyambirira ndipo pasanapezeke Allah panalibe chilichonse, komanso iye ndiwomaliza pambuyo pake palibe chilichonse, Allah akunena kuti (132)“ Iye alibe chiyambi, wamuyaya, woonekera, wobisika kwambiri (saoneka) ndipo iye ndi wodziwa chilichonse” Surat: Al Hadid: 3)ndithu nthawi ili ngati malo sizingaike malire a Allah, ndipo nthawi ndi chimodzi mwa zolengedwa za Allah, kotero zolengedwa sizingaike malile kapena kumuzungulira mlengi wake, Allah ali ndi mbiri zonse zabwino ndi zokwanira, apa tikuyenera kuchenjera ndikulandira langizo (wasiyyah) la mtumiki (SAW) lomwe Abu Hurairah adamumva mtumiki akunena kuti: “Satana amatha kumufikira mmodzi wa inu ndikumamufunsa kuti kodi ndani adalenga chakuti? Nanga chakuti anachilenga ndi ndani? Mpaka amafika pofunsa kuti: ndani analenga mbuye wako? Pakafika pamenepa, iye adzitchinjirize mwa Allah kenako aziiwale (zomwe amafunsidwa ndi satanazo)” (Bukhar 3276), kudzitchinjiriza mwa Allah ndi kutembenuzira maganizo amwana ku zinthu zina mosakhala mwachindunjiku, ndicholinga choti asapitirize mafunso amenewa, nakonso ndi umodzi mwa mitundu yakuyankha kofunikira pa nkhani imeneyi, pomwe kutembenuzamaganizo a mwana ndi kuwatalikitsa ku zimenezi si kuti ndi chifukwa choti ulibe yankho ayi, koma kutseka molowera manong’onong’o a satana.

Funso Kodi Allah ndi wamwamuna kapena wankazi?

Tikuyenera kuzitalikitsa nzeru za mwana kuti zisamaganizire kwambiri za maonekedwe a Allah, ndipo tiziongolere nzeru zake kuti ziziganizira zinthu zomwe zingamubweretsere phindu, apa tsopano zidzakhala bwino kumuuza momveka kuti kukhala mwamuna kapena mkazi ndi zinthu zosiyanitsira magulu ndi mitundu ya zolengedwa za moyo, izi ndi zina mwa zomwe Allah anazipatsa zolengedwa zake, Allah akunena kuti: “ Ndipo iye ndi amene adalenga mitundu iwri: chachimuna ndi chachikazi”. (Surat Al Nnajim: 45) pomwe Allah ali pamwamba pa onsewo.
komanso kuli zolengedwa zina zomwe sizimalowa nawo mmagulu amenewa, monga: angelo, kumwamba, mitambo, mphepo ndi madzi, zimenezi sizimatchedwa zazimuna kapena zazikazi, choncho ngati zikutheka kupezeka zolengedwa zina zosalowa nawo mmagulu amenewa, nde kuti Allah ndi amene akuyenera kwambiri kusapezeka nawo mmagulu amennewa: “Palibe chilichonse chofanana ndi iye, iye ndi wakumva zonse ndiponso woona zonse” (Surat Shura: 11).

Funso KODI NCHIFUKWA CHIYANI TIMAKHULUPIRIRA KUTI ALLAh ALIPO? NANGA TINGATSIMIKIZE BWANJI ZIMENEZI?

Kukhulupirira mwa Allah ndi chibadwa cha munthu wina aliyense chimene palibe yemwe angachitsutse ndipo ma umboni oti Allah alipo ndi ochuluka zedi, ndipo anthu adakatulukirabe ma umboni pamwamba pa maumboni ena, wina aliyense mwa anthuwo molingana ndi mbali yake ya maphunziro imene akufufuza, ndipo umboni wa chibawa cha munthu umatsimikizira kuti Allah alipo, Allah akunena kuti: “Dzikakamize wekha kuchilengedwe chimene (Allah) adalengera anthu,( ichi ndi chipembedzo cha chisilamu chomwe nchoyenerana ndi chilengedwe cha Munthu)”. (Surat Al Rum: 30) tonsefe timamva mumtima mwathu kuti muli mphamvu ina yake yomwe imauuza mtimawo za ukulu, mphamvu ndi chisamaliro cha Allah pa ife, pomwe maumboni okhudzika ochokera mmaphunziro akutsimikiziranso kuti pa dziko pano pali dongosolo la kuya ndi la mtengo wapatali, ndipo dongosolo limeneli pali amene analiika; chifukwa zolengedwa zonsezi ndi ndani anazipezeketsa?

Kutheka kuti zinangopezeka mwangozi popanda wozipezeketsa,ngati zili choncho nde kuti palibe angadziwe mmene zinapezekera zinthu zimenezi, chimenecho ndi chiyembekezo choyamba.Pomwe chiyembekezo chachiwiri ndi choti: zinthu zimenezi zinadzipezeketsa zokha ndipo zimadziyang’anira zokha,ndipo chiyembekezo chachitatu ndi chakuti: pali amene anazipezeketsa ndi kuzilenga.

Ndiye tikayang’ana ziyembekezo zitatu zonsezo, tipeza kuti chiyembekezo choyamba ndi chachiwiricho nzosatheka, zikatero nde kuti choyambacho ndi chimene chingakhale choona komanso chomveka, zoti pali mlengi yemwe adazilenga(Allah),ndipo izi ndi zomwe Allah adazinena mu Qur’ani ponena kuti: “ Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha, kodi iwo ndi amene adalenga thambo ndi nthaka? Koma iwo sakhulupilira kweni kweni”. (Surat Al Tur: 35 -36).

Ndipo ena mwa maumboni osonyeza kuti Allah alipo ndi izi: kuyankha kwa Allah ma dua(mapempho)a anthu, ukatswiri wa kalengedwe ka mitambo ndi nthaka, Allah akunena kuti: “Ndithudi mukalengedwe kakumwamba ndi dziko lapansi ndikusinthana kwausiku ndi usana, ndizisonyezo(zoti kuli mlengi wa zimenezi) kwa eni nzeru”. (Surat Al Imran: 190), komanso poona ukadaulo wa kalengedwe ka munthu, Allah akunena kut: “Ndimwainu nomwe kodi simuona?”.(Surat Adhariyat: 21). Ndi kalengedwe ka nyenyezi, mapiri, zinyama, ndi zina zotero, zonsezo zimasonyeza ukatswiri wa Mulungu pa zolenga zake.

Ndithu zizindikiro zoti Mulungu alipo zili pali ponse: pa dzikoli, m’mitima kapena mmatupi (a anthu ndi zinyama), ndizipatso zonse zikusonyeza kuti kuli Mu-lungu m’modzi wayekha (yemwe adazipezeketsa zonsezi) ndipo kupezeka kwa zolengedwa zonsezi kukusonyeza kuti kuli ndi cholinga chapamwamba zedi chomwe Mulungu adazilengera ndipo zonsezo zimapembedza Mulungu (Allah) yekha yemwe alibe chophatikizana nacho (133).

Ndizothekanso kumusimbira mwanayo nkhani ya Abu Hanifah (R.a) atamupempha anthu ake kuti awatsimikizire zoti kuli Tauhid ya Rububiyyah (zoti Mulungu yekha ndi amene amalenga ndi kumasamalira zomwe walengazo) Abu Hanifah anati kwa anthuwo tisanakambe nkhani imeneyi tandiuzeni zachombo chomwe chimadziyendetsa chokha pa mtsinje wa Dijlah (Tigris) nichikatenga chakudya ndi katundu wina pachokha nabweleraso pachokha, ndikumaimanso chokha kenako ndi kutsitsa katunduyo chokha ndikumabwelera, zonsezo chombocho chimapanga chokha popanda wochiyendetsa komanso wochiyang’anira (Tandiuzeni kuti zimatheka bwanji zimenezi?) ndipo iwo adati zimenezo sizingatheke komanso sizidzatheka mpaka kalekale, Abu Hanifah adat: ngati sizingatheke zimenezo pa Chombo; kuli bwanji dziko lonseli m’mene lakuliramu kuyambira kumwamba mpaka pansi pano! (134) Ndithu nzosatheka kuti kalengedwe kaluso kadziko limeneli kakhale kopanda Mlengi wakutha kwambiri komanso wozindikira zedi.

Nzothekanso kumufunsa mwana kuti kodi ukamamva kupweteka m’mimba siuja umazindikira kuti uli ndi njala, kenako ndikumafunafuna chakudya wekha wekha kuti uthetse njalayo? Komanso ukamva ludzu siuja iwe umafunafuna chakumwa chimenechingathetse ludzu limeneli?ndipo ukanunkhitsa fungo labwino siuja umasangalatsidwa nalo iwe? pomwe ukamva fungo loipa siuja umanyasidwa? Komanso ukamaona maluwa, mitambo ndi chilengedwe chomwe chatizungulira, kodi simumasangalatsidwa nacho ndi kukupatsa chimwemwe?
Chimodzimodzi m’bale wanga wolemekezeka tonsefe timazindikira mwaife tokha kuti timafunikira wachikulire kwambiri kuti tizimudalira nthawi iliyonse tikafuna kuti tipeze mpumulo ndi chitetezo, chifukwanthawi imeneyi timayamba kubanika ndi kudandaula; ndithudi mwaife tokha mwachidziwikireni kuti timathawira kwa Mulungu ndikumupempha iye, ndipo tikakhala pa mtendere timamutamanda iye pa mtendere umeneu.

Funso Kodi Mulungu amamva, kuona kapena kulankhula ngati ife?

Ndithu Mulungu amalankhula, kumva komanso kuona, Mulungu akunena kuti: “Ndithu Mulungu wamva mau a (mkazi) akubwezerana bwezerana nawe(mau) pazamwamuna wake” (Surat Al mujadilah: 1). adanenaso kuti: “Mulungu adati musaope ndithu ine ndili nanu pamodzi ndikumva ndiponso ndikuona” (Surat twaha: 46) adatiso: “Ndithu iye (Mulungu) akuona zonse zimene muchita” (Surat Hudu: 112), koma singati m’mene ife timalankhulira kapena kumvera ndikuonera ayi, chifukwa Mulungu ndiwosiyana ndi zolengedwa zake, iye amamva mau ngakhale atakhala mauwo alankhulidwa mobisika chotani, amaona chilichonse angakhale chitatalikira motani, Mulungu amaona ndi kumva chilichonse koma kuona ndi kumva kwakeko sikumafanana ndi kumva kapena kuona kwa zolengedwa zake chifukwa kuona ndikumva kwa zolengedwa ndi kofooka komanso kopunguka chifukwa Mulungu akulankhula Kunena kuti: “Palibe chilichonse chofanana ndi iye, iye ndiwakumva zonse komanso woona zones”. (Surat Ashura: 11).
Ndipo ndibwino kuzilumikiza zimenezi ndi khalidwe la chindunji, monga kufunsa kuti: ngati Mulungu ali wakumva ndi kuona mwamphamvu, kodi tikuyenera kukamba zomwe sizingamusangalatse ndiye atione tili pakaonekedwe komwe iye samakafuna?! (135).

Funso Kodi Mulungu samva njala kapena ludzu?

Mulungu (mwini mphamvu ndi ulemelero wonse) ali ndi mbiri zokwanira zokha zokha ndipo alibe mbiri iliyonse yopunguka. Ndithu njala ndi ludzu ndi zizindikiro zakufooka ndipo sizifunikira kumpatsa Mulungu, komanso Mulungu safuna chakudya kapena chakumwa (136); chifukwa Mulungu ndi amene analenga chilichonse kotero safunikiranso chilichonse mwazimenezo, kotero iye akanafunikira chinthu china chake sakanakhala Mulungu. Inde Mulungu ndi chikhomo samadya komanso safunikira chakudya ndi chakumwa, iye alibe nazo ntchito zimenezo, komanso iye ndi amene amapemphedwa ndi zolengedwa kuti azithandize, monga kuzidyetsa, kuzimwetsa ndi kuzipangira zokhumba zake.

Ndizothekanso kumuuza mwanayo kuti: ndithudi Mulungu palibe chomuyerekezera ndi zolengedwa zake, ndipo sizoona kuti chilichonse chomwe ife tingapange ndi kuchitulukira chingakhale mbiri yathu kapena maonekedwe anthu ayi, si choncho? Mulungu samamva njala kapena ludzu, ndilorenindikufunseni funso: kodi amene amapanga njinga ndi ndani? Iye adzayankha kuti “kampani yopanga njinga”; zilibwino kwambiri, tabwera mwana wanga tilingalire limodzi kuti njinga izimufunsa yemwe anaipanga kuti: umadya chiyani? Umamwa chiyani? Ungayiyankhe chiyani? Ndingaiuze kuti zimenezo sizikukukhudza, upin-dula chiyani ukadziwamo, kodi yankho lako lizaonjezera chiyani ku ntchito yake yeniyeni yanjinga yoyenda mwachangu ndi mopanda ulesi, chabwino (zilibwino kwambiri), chimodzimodzi –mwana wanga – Mulungu anatilengera ntchito yochepa ngatim’mene Allah akunenera: “Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza” (surat adhariat: 56). Choncho mafunso amenewa sangatithandize kupeza ntchito ina yoonjera pantchito yomwe Mulungu anatilengera, koma mmalo mwake mafunso amenewa atisokoneza nzeru zathu kuti tisathe kugwira ntchito yomwe adatilengera. Kodi nanga njingayi idzalunjika liti kwa ifeyo kutipempha thandizo? Ikazaonongeka china chake, ndithu iyo idzalunjika kwa okonza kuti akakonze choonongekacho, chimodzimodzi ife timalunjika kwa Mulungu pomupempha tikaona kuperewera pakupembedza kwathu, kapena likatigwera vuto lina lake.

Funso Kodi mphamvu za Mulungu ndi zochuluka bwanji?

Ndithu ife tikamanena zamphamvu kapena kuthekera komwe kuli koperewera; ndiye kuti tikutanthauza mbiri yofooka, chifukwa pothera mphamvu imeneyo ndipamene padzayambire kufooka, ndipo kufooka sikumakhala pa Mulungu choncho kuthekera kwa Mulungu ndikopanda malire ndipo palibe chomwe chingamufoole iye kapena kumulepheletsa, Mulungu akunena kuti: “Kodi siukudziwa kuti Mulungu ngokhonza chinthu chilichonse” (surat bakara: 106) ndipo akafuna chithu amangoti “chichitike” ndipo chimachitika.
Mulungu ndi wakutha chilichonse; chifukwa iye ndi Mlengi wachili chonse, sichingamukanike chili chonse chadziko lapansi ndi kumwamba komwe.

Pomwe kuthekera kokhala ndi malire ndikwa zolengedwa, chifukwa kumeneko ndikuthekera kochita kulengedwa. Pomwe kuthekera kwa Mlengi; kulibe malire kapena kupunguka. Choncho; Mulungu yekha ndi amene akuyenera kupembedzedwa ndi kupemphedwa; chifukwa iye yekha ndi amene ali ndi kuthekera koyankha ndikuthandiza zofuna zazolengedwa, kuwadyetsa ndikuwakwanilitsira zofuna zawo komanso kuyendetsa zichitochito zawo (137).

Funso Kodi Mulungu amakhala kuti nanga ndi wamkulu motani?

Pambuyo poti mwana wamvetsa pansi pansi zoti Mulungu ndi amene adamulenga komanso kuti Mulungu amakonda ana kwambiri, ndikuti iye anamupatsa mwanayo mitendere yochuluka, ndizotheka nthawi imeneyo kumulongosolera kuti Mulungu alipo ndipo amapezeka kumwamba, Mulungu akunena kuti: “Kodi muli m’chitetezo kwa amene ufumu wake uli kumwamba” (Surat al muluku: 16), iye ( Mulungu) alikumwamba koma kuzindikira kwake kuli paliponse, Mulungu akunena kuti: “Ndipo iye alinanu paliponse pamene muli” (Surat Al Hadid: 4), ndipo si zoyenera kwa ife Kunena kuti Mulungu ali pali ponse ayichifukwa kutero zizatanthauza kuti Mulungu ali mkati mwachili chonse, zimenezo sizoona ayi; ndithu ife timagwiritsitsa zomwe zili muchiphunzitso, Mtumiki (saw) anamufunsapo kapolo wachikazi kuti: “Kodi Mulungu amakhala kuti?” iye adati: “kumwamba”, Mtumiki (saw) adati “nanga ndine yani?” iye adati: “Mthenga wa Mulungu”, Mtumiki adati: “Mmasuleni ukapolo chifukwa iye ndi wokhulupirira”. ( Muslim -537).

Ndiye ngakhale iye amakhala kumwamba komabe amakwanitsa kutiona ndikutimva malo ali onse, ndipo timutsimikizire mwanayo nthawi zonse kuti Mulungu amamuona iye nthawi zonse, umeretse chimenechi mu mtima wamwana ndipo chikhale chomulondera iye (mlonda wake), pomwe zokhudza kukula kwake: Mulungu wapamwamba mwamba asafanizidwe ndi cholengedwa chilichonse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa chili chonse, kuposa zolengedwa zonse moti pakapezeka zolengedwa zazikulu zikulu ndithu Mlengi wake ndi wamkulu kuposa izo; ndipo iye ndi amene adzazule mapiri, ndi kugwedeza Nyanja, amawalamula madzi kuti azilowa munthaka, ndipo zonse zomwe zimachitika padziko pano zimachitika muchilamulo chake ndi chifuniro chake, ndithu Mlengi safuna thandizo lochokera kuzolengedwa zake, thambo ndichimodzi mwa zolengedwa za Mulungu ndipo kupezeka kwake (Allah) sikuti kwagona pa kupezeka kwa thamboko ayi, ndipo iye sapeza phindu lililonse kuchokera ku thambolo, chifukwa Mulungu ndi wolemera kwambiri kuposa wina aliyense ndipo safuna thandizo la chilichonse (138).

Funso KODI ZIMATHEKA BWANJI IFE ALLAH AMATIONA POMWE IFE IYE SITIMAMUONA?

Ndithu maso omwe Mulungu anatipatsa pa dziko lapansi pano ndi ofooka sangathe kuona zochuluka; pa chifukwa ichi mudzaona munthu akugwiritsa ntchito zipangizo zoonera zinthuzazing’onozing’ono (microscope) ndi zipangizo zina zokulitsira zinthu, ndiye ngati munthu akulephera kuziona zinthu zolengedwa, kusamuona Mulungu kudzakhala koposa,ndithu kuthekera kwa munthu pa dziko la pansi lino sikungamuthandize kuti amuone Mulungu,ife sitingakwanitse kumuona Mulungu koma timamukhulupirira, timakhulupiriranso kuti Mulungu ndi wachifundo komanso amatikonda, ndiwamphamvu komanso ali ndikuthekera kopanga chilichonse, ndipo amadziwa chilichonse, ndiponso akudziwa kuti ife pa nthawi ino tikukambirana za iye,ndithu Mulungu safanana nafe kutalitali, choncho iye amationa tonsefe nthawi imodzi ngati mmene zimakhalira munthu akakwera pamwamba pa nyumba yosanjikizana amatha kumawaona anthu onse omwe ali munsewu pomwe iwo samamuona iye,choncho Mulungu amationa koma ife sitimamuona iye.

Ndithu pali zinthu zambiri zomwe sitingathe kuziona koma izo zilipo, ndipo timuuze mwana kuti: ndithu maso athuwa sangathe kuona zinthu zonse ayi, ife sitimatha kuwaona mawu ngakhale timawamva, sitingaone mphepo ngakhale imatikhudza (imatiomba), ndiye maso athuwa sangathe kumuona Mulungu pa dziko pano, koma ku Jannah – mu chifuniro cha Mulungu- tikakhala kumeneko ndi maso abwino kwambiri omwe akakwanitse kumuona Mulungu wapamwambamwamba, choncho Mulungu akulankhula kunena kuti: “Maso samufika iye (samuona); koma iye amawafika maso (amawaona pamodzi eni masowo). Iye ngodziwa zobisika kwambiri ndi zoonekera”. (Al ani’am:103).

Funso KODI ALLAH AMAKWANITSA BWANJI KUWAONA ANTHU ONSE KUMACHITA KUTI IWO NDI OCHULUKA KWAMBIRI?

Kuti tithe kuliyankha funso limeneli, timutenge mwanayo tikaime naye pa msewu, numufunsa kuti: uziwayang’ana anthuwo kenako undiuze kuti waona angati, tiwerenge limodzi anthu omwe ungawaonewo, kenako tikwere pa nyumba yaitali ndikumuuzanso kuti aziwerenga omwe akuwaona, kenako tikwere naye nyumba yaitali kwambiri ndikumuuzanso kuti aziwerenga anthu omwe akuwaona, kenako timupatse magalasi kuti azitha kuwaona anthuwo ndi kuwawerenga bwinobwino.

Kudzera mu chitsanzo chimenechi, tidzatha kumuwalitsira mwanayo kuti ndithudi ife sitingathe kuyeza bwino zinthu patokha pogwriritsa ntchito miyezo ya umunthu wathu, choncho timufotokozere iye kuti kuthekera kwa Mulungu ndi kwa kukulu kwambiri kuposa kuthekera kwa zolengewa zake zonse,ndipo tiike mu nzeru za mwanayo nthawi zonse mawu awa: “Kodi siukudziwa kuti Mulungu ngokwanitsa kupanga chinthu chilichonse”. (Baqarah :106).

Tingathenso kumufunsa funso lokhudzika ili: kodi umakhulupilira kuti nyerere zimationa ife m’mene tilili kapena zimangotiyerekeza kapena zimangoona zithunzi? Iye adzayankha kuti nyerere imangokwanitsa kuona mbali chabe yaying’ono kwambiri yachala chathu chachikulu chakumiyendo, mwinanso ingathe kuganizira kuti chalacho ndi phiri kwa iyo. Chabwino, nanga ukuganiza kuti nyerere ingathe kufunsa kuti umakwanitsa bwanji kutiona ife tonse pakamodzi? Yankho lako lidzakhala lonena kuti: zimenezo ndi zachikhalire: chifukwa zikugwirizana ndi kuthekera kwako komwe Mulungu anakulengera.

Nyerere kuthekera kwake ndi kochepera, ndipo patha kupezeka nyumba zochuluka za nyerere m’malo osiyana siyana padzenje limodzi, ndipo nzophweka kwa iwe kuwaona malo onsewa nthawi imodzi, pomwe nyerere ndikuthekera kwake kochepa kuja siingathe kuona momwe iwe ungaonere, ndiye monga m’mene tagwirizanira kale kuti Mulungu safanana ndi china chilichonse, komanso kuti iye amatha chilichonse, choncho sizoyenera kumufunsa Mulungu ndikuthekera kwathu kochepaku zinthu zoti kwa iye ndizosakaikitsa, chifukwa kuthekera kwa Mulungu ndi kwakukulu kwambiri kuposa kuthekera kwa zolengedwa zonse, chifukwa Mulungu akunena kuti: “Kodi sukudziwa kuti Mulungu ngokhonza (ngokwanitsa) chinthu chilichonse” (Surat AlBakara: 106).

Funso Kodi Mulungu amawaonanso anthu ndimum’dimamomwe? KODI ALLAH AMAKWANITSA BWANJI KUTIONA TIKAKHALA MNYUMBA ZATHU, MAKOMO NDI MAWINDO ALI OTSEKEDWA?

Tingathe kumupatsa mwana filimu kuti aonere makamaka mwa ma filimu omwe amaonetsa asilikali a pamtunda omwe amaona pogwiritsa ntchito ma galasi oyang’anira ukafika usiku,ndipo timuonetsenso ma filimu oonetsa zina mwa zinyama ndi mbalame zomwe zimaona usiku, komanso ena mwa ma filimu omwe amaonera ndi masewero omwe amasewera mumatha kupezeka zipangizo zojambulira monga (laser) zomwe zimaonetsa za kuseli kwa zinthu komanso zimationetsa zinthu zomwe zili mu mdima, pambuyo pake timuuze mwanayo kuti:ukumuona munthu (cholengedwa) wofooka mmene akumakwanitsira kuona mu mdima nthawi zina? Kuli bwanji mbuye wathu amene anamulenga munthu ameneyu ndi zolengedwa zonse (139), ngati Mulungu anatipatsa kuthekera kopanga zachilendo zimenezi, kodi angalephere- iye amene ali wakutha ndi woyang’anira – kupanga zimenezo? Kumachita kuti ndi wakutha komanso wamkulu kwambiri, ndipo kuthekera kwa Mulungu palibe amene angakutchinge kapena kukulepheretsa.

Timuonetse mwana zithunzi zakuchipatala kenako timufotokozere kuti ndithu munthu yemwe Mulungu adamulenga adakwanitsa kuliona fupa litatsekedwa bwino bwino pogwiritsa ntchito chipangizo cha x-ray, kuli bwanji Mbuye wathu yemwe adalenga munthuyo? Ndithudi Mulungu amationa tikakhala m’manyumba mwathu titadzitsekera makomo onse , ndithu Mulungu safanana ndi chili chonse, iye salingati munthu yemwe zipupa zimamulepheretsa kuona, Mulengi sangakhale ngati cholengedwa; chifukwa Mulungu ndiwakutha chilichonse, ndipo ndizoyenera kulilumikiza yankho limeneli ndi zichito chito zamwanayo polimbiktsa mbali yakuzilondera ndikuchimva kukoma chipembedzo mu mtima mwake mwanayo (140).

Funso KODI ALLAH AMADZIWA BWANJI NTCHITO ZATHU? NANGA AMAKWANITSA BWANJI KUYANG’ANIRA ANTHU ONSE?

Mwana akuyenera kudziwa nthawi zonse kuti Mulungu ali ndi mbiri zabwino ndizokwanira zokha zokha, adziwenso kuti kuthekera kwa Mulungu kulibe malire, iye ndi wakutha zedi, Mulungu akunena kuti: “Kodi sukudziwa kuti Mulungu ngokhonza (ngokwanitsa) chinthu chilichonse?” (Surat Al Bakara: 106), ndiye chifukwa chakuti Mulungu ali ndi kuthekera kwa kukulu palibe chimene chimamukanika padziko lapansi pano ndi kumwamba komwe, ndizosatheka kuyerekeza kuthekera kwa Mulungu ndi kuthekera kwa zolengedwa, kuthekera kwazolengedwa ngakhale kungakule bwanji, kuthekera kwa Mulungu kudzakhala koposa kwambiri. Pofuna kuyandikitsa tanthauzo limeneli: nzotheka kumpatsa chitsanzo chazojambulira video (video camera) m’mene chimakwanilitsira kujambula ndikusunga kakang’ono ndikakakulu kena kalikonse komwe diso lake (camera) laona, ndipo Mulungu ali ndi kuthekera kwakukulu kwambiri koposa chilichonse, iye amatha kuyang’anira anthu onse nthawi imodzi, chifukwa kuthekera kwake kulibe malire, ndipo Mulungu amadziwa ndipo kudziwa kwake ndi kokwanira komanso kopanda malire pa china chilichonse (141).

Tithanso kumupatsa chitsanzo ichi: tiyerekeze kuti pali kampani yayikulu ukufuna uziyang’anira ogwira ntchito mmenemo, ndipo mwawayikira ma kamera iwo asakudziwa, ndipo mwayamba kuwayang’anira mwachinsinsi kudzera pa ma sikilini (sreen/video monitor) oonetsa kalikonse kochitika pa kampaniyo nthawi imodzi, ngati kapolo kapena cholengedwa chofooka chomwe Mulungu adachilenga chikukwanitsa kupanga zimenezo, ndiye akalephere yemwe adalenga kapolo ameneyo ndicholengedwa chimenechi kuwaona akapolo ake onse nthawi imodzi?.

Funso Kodi Nchifukwa chiyani munthu amamwalira ndipo Mulungu samwalira? KODI ALLAH AMANDIKONDA NGATI MMENE INE NDIMAMUKONDERA?

Ndithu infa ndi chikonzero cha Mulungu chomwe anakonzera zolengedwa zake Mulungu akunena kuti: “Chamoyo chilichonse chidzalawa infa,kenako mudzabwezedwa kwa ife”. (Al Akabut: 57), ndiye kufa kwa munthu ndichiyambi cha moyo uli nkudza, ndipo umenewo ndiwo moyo umene uli wofunikira kwambiri.

Ndithu infa ndi chizindikiro chosonyeza kufooka chomwe wamoyo wolengedwa aliyense chidzamupeze, ndiye kufooka sikumapezeka mwa mulungu, chifukwa Mulungu sadalengedwe ndipo sadzamwalira, pomwe munthu ndiwolengedwa ndipo amamwalira, ndithu umoyo wa Mulungu sufanana ndiumoyo waife, umoyo waife umatha ndi ifa, ndipo zolengedwa zonse zidzamwalira, adzatsale ndi Mulungu yekha, ndithu moyo wa Mulungu ndiwokwanira ndipo ukuyenera kukhala ndi mbiri zonse zakukwanira, makamaka mbiri yoti iye ndiwa moyo yemwe sadzafa (142).

Mulungu ndi wokhululuka ndi wachifundo amawakonda anthu abwino okhazikika ndi onena zoona, Mulungu akunena kuti: “Allah awakonda iwo, nawonso amukonda Allah yo” (surat Al Maida: 54), ndipo zizindikiro zachikondi cha Mulungu pakapolo wake ndi izi: Mulungu amawalemekeza iwo ndikuwachengetera, ndikuwayendetsera zichito chito zawo, kuwadyetsa ndi kuwakhululukira, ndipo aliyense amachikhudza chifundo cha Mulungu ndi ulemelero womwe Mulungu anamupatsa, ndipo Mulungu amamukonda kapolo wake yemwe amamumvera iye ndikudziyandikitsa kwa iye ndipo amagwiritsa ntchito mphamvu yake yonse kuonetsa chikondi kwa Mulungu; monga kusamala swala, kuchitila ubwino makolo, kupereka chaulere, kuchitira ubwino anthu, kunena zoona, kuwerenga Quru’an, kumutchulatchula Mulungu, ndi ntchito zina zabwino, yemwe angapange zimenezi Mulungu wapamwamba mwamba amamukonda.

Back to top button